UPAMWA WA MAPEMPHELO A SWALATI (MAPEMPHELO A KA NSANU PA TSIKU )

UPAMWA WA MAPEMPHELO A SWALATI (MAPEMPHELO A KA NSANU PA TSIKU )

 Ndithu upamwamba wa mapemphelo ndi woti  , munthu akakhala kuti iyeyo akupembedza Mulungu kweni kweni choonadi ndithu . ndithu Allah munthu uja amakhala kuti  kudzela mu swalati mo kummapanginsa kuti zoipa zonse za pa Dziko  la pansi azitalikinsidwa ndithu , ndithu moti m,bale wanga  ngati mudzamuone kuti wina akumapembela koma ndi kumapitilidza zoipa mudzangodziwa kuti mkulu ameneyo swalati pa manso pa Allah siukufika kwa Mulungu ndithu chifukwa swalat ndi imene ikuyenela izikutchinjila zoipa osati munthu akuswali koma kumapitilidza zoipa ayiiiiiiiii m, bale wanga  Msilamu .

 

Komanso ubwino wa swalat ndi oti swalati imapanginsa kuti munthu azikhala opanda mantha  kwa china chili chonse kupatula Mulungu wake yekha ndithu ( za njala , za mchuma , za umphawi kaya kuludza kwa chuma ,ndi mabvuto ena mwa otelo ndithu ndithudi opemphela saopa komanso  sakhala ndi nkhawa olo ndi madandaulo ndithu .)

 

AttachmentSize
File 6570-f-chichwa.mp438.53 MB