Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 8

Imam Baqir (a.s) adanena kuti: والله لَمَوتُ عالمٍ أحبُّ إلى إبليس من موت سبعين عابداً. Ndikulumbira mwa Mulungu kuti imfa ya munthu ophunzira zachipembedzo ili bwino kwambiri pamaso pa satana kuposa imfa ya akapolo okwana 70. - Satana amasangalala ndi imfa ya munthu ophunzira za chipembedzo chifukwa choti amakhala ndi mpata owasokoneza anthu omwe atsala opanda owakumbutsa zachipembedzo komanso Mulungu. - Munthu ophunzira ali ngati nkhokwe yachipembedzo kotero iye akafa chipembedzo chimasawuka ndipo izi zimakondweretsa satana. - Chimodzi mwa ziwonetsero za mapeto adziko lapansi ndichoti anthu adzakhala otalikirana ndi anthu ophunzira zachipembedzo. Azidzati akamuwona munthu ophunzira zachipembedzo mitima yawo simakondwa ayi, anthu oterewa adziwe kuti ali limodzi ndi satana.

AttachmentSize
File a168ef9cef1a10831710cbb3aca485b4.mp418.19 MB

Add new comment