Anthu m\'magawo atatu

Mukuyang\'ana kwa chipembedzo cha Chisilamu anthu akugawidwa m\'magawo atatu: 1) Mujtahid 2) Muhtwat 3) Muqalld. Magawo awiri oyambawo ndi ovuta kwambiri ndipo ndi anthu ochepa omwe amatha kufika pa magawo amenewa. Koma anthu ambiri pano padziko lapansi ndi ma Muqallid, kutanthauza kuti amatsatira munthu yemwe ali ozindikira yemwe muchipedzo amatchedwa Mujtahid. Ndipo kutsatira munthu ozindikirayu ndi zokakamizidwa (Wajib) chifukwa ndi nzeru zomwe zikutilamula kuteroko ndipo izi zikuchitika pa Ahkam ndi ntchito za chipembedzo. Koma pankhani ya chikhulupiliro ndi zoletsedwa kutsatira munthu wina ndipo aliyense ayenera kupeza umboni mwa iye yekha pa zikhulupiliro pogwiritsa ntchito nzeru zake

AttachmentSize
File 241da25e22d3c815375de20abc31db81.mp49.14 MB

Add new comment