Zodabwitsa zomwe zidachitika pambuyo pakuphedwa Imam Husain(a)1

Zodabwitsa zomwe zidachitika pambuyo pakuphedwa Imam Husain(a)1

 

chidachitika   ndi chani  pambuyo  pakuphedwa  kwa  Imam  Husain(a) tsiku  la  Ashura?
Mashia  amakhulupirira  kuti kusankha  kwa  mtsogoleri (Imam) pambuyo  pa  Mtumiki(s.a.a.w) kuli mmanja  mwa  Mulungu  ndipo  munthu alibe  chilolezo  cholowerera  pa nkhaniyi. Monga  momwe  zilili  kuti  kusankhidwa  kwa  Mtumiki  kuli  mmanja  mwa  Mulungu  motero  munthu  alibe  mphamvu  yolowerera  pankhaniyi.
Mu Quran  muli ma aya  omwe  akuikira  umboni  za  nkhaniyi: Mulungu  pankhani  ya  utsogoleri (Imam)  wa  Ibrahim  akunena  kuti:
إِنِّي جاعِلُكَ لِلنَّاسِ إِماما . البقره / 124
Ine  Mulungu  ndikukupanga  iwe  kukhala  mtsogoleri (Imam) wa  anthu.
Komanso  Mulungu  akunena  kuti:
وَهَبْنَا لَهُ إِسْحَاقَ وَ يَعْقُوبَ  وَ كلاً جَعَلْنَا نَبِيًّا . مريم / 49
Ife  tidampatsa  Ibrahim  Ishaqah  ndi  Yaqub (yemwe ndi mwana wa Ishaqah) ndipo  tidapanga  onse  awiri  kukhala  atumiki.
Mu  ma aya  amenewa  taona  kuti  kusankhidwa  kwa  Ibrahim  kukhala  mtsogoleri  kuli mmanja  mwa  Mulungu  komanso  kukhala  kwa  Ishaqah  ndi  Yaqub  atumiki  kuli mmanja  mwa  Mulungu,  palibe  aya mu Quran yomwe  ikunena  kuti  utumiki  ndi  utsogoleri  uli  mmanja  mwa  anthu.
Mashia  amakhulupiriranso  kuti  monga  momwe  Mtumiki  amayenera  kuti  aonetse  zozizwitsa  pofuna  kutsimikizira  za  utumiki  wake, mtsogolerinso  ayenera  kukhala  ndi  zozizwitsa  kuti  atsimikizire  utsogoleri  wake,   kupanda  kutero  ndiye  kuti  utsogoleri  wawo  ukhala  osavomerezeka  ndi  anthu.
Ahlubait(a)   amene  ali  atsogoleri (ma Imam)  pambuyo  pa  Mtumiki(s.a.a.w)  adali ndi  zozizwitsa  zimenezi   ndipo  kuchokera  mmenemu  ndi  momwe  anthu  amamvera  ndikukhulupirira  zokamba  zawo  komanso  kuvomereza  za  wu Imam  wawo.
Imam  Husain(a)  yemwe  ndi  Imam  wachitatu  mu mathihab  a chishia  adali  ndi zozizwitsa  zambiri  munthawi  ya  umoyo wake  angakhale  pambuyo  pa  imfa  yake  zomwe  zikusonyeza  kuti  munthuyu  adali  mtsogoleri  weni-weni  ndi osankhidwa  ndi  Mulungu  komanso  Imam  oyenera  pambuyo  pa m’bale  wake  Hasan(a). Choncho  ndizosatheka  kuti  Mulungu  apereke  zozizwitsa   zimenezi  kwa  anthu  omwe   sali  oyenera  pa udindowu  ndipo  ndi  zozizwitsa  zimenezi  ndikusocheretsa  nazo anthu.(Tithawire  kwa  Mulungu  ndi  mau  ngati  amenewa).
Pano  mwachidule tikufuna  kuti  tineneko  zina  mwa  zozizwitsa  zomwe  zidachitika  pambuyo  pakuphedwa  kwa  Imam  Husain(a).  Zodabwitsa  zomwe  zikuchokera  kwa  munthu  yemwe  nzeru   zidagonja  ndi  iye  pa zochitika  zazikulu  zimenezi. Zosakaikitsa  kuti  zodabwitsa  zimenezi  zili  zokwanira  kuti  choonadi  ndi  chilungamo  chionekere  kwa  munthu  yemwe  akufuna  chiongoko. Koma  kuti  munthu  athe    kumvesetsa  zodabwitsa  zimenezi  ayenera  kuchotsa  mumtima  mwake  nkhani  yatsango ndikunyoza  kuti  athe kuona  nkhaniyi  ndi  mtima  wake  oyera.
Pomwe  mashia  akutsatira  Imam Husain(a)  yemwe  ndi tsogoleri  ochokera  kwa  Ahlubait(a) ndikukhulupirira   zodabwitsa  zake, pali  anthu  ena  omwe  safuna  kutsatira utsogoleri  wa  mwana  wa Mtumikiyu  koma  mmalo  mwake  akutsatira  anthu  omwe  ali  adani  a akunyumba  ya  Mtumiki(s.a.a.w). 
Tikufuna  kutchula   zodabwitsa  zimenezi  kuchokera  mu mabuku  ndi  mashaikh  odalilika  kuti  ukhale  umboni  kwa  anthu  onse  ndikuti  anthu  okanira  asakhale  ndi  mpata  wina ulionse  okanira.