Zionetsero za Husain(a) mu Quran 4

Zionetsero za Husain(a) mu Quran 4

Mulungu  subuhanah  wata’ala  akunena  mu Quran yolemekezeka kuti: 

يا أيتها النفس المطمئنة * ارجعى إلى ربك راضية مرضية * فادخلى فى عبادى و ادخلى جنتى؛   . الفجر: 27- 30
E!  iwe  mtima  odekha  ndikukhazikika, bwerera  kwa  mbuye  wako  uli  osangalala  komanso  osangalalidwa  ndi Mulungu, lowa  mugulu la  akapolo  anga, lowa  mu mtendere  wanga.
Kodi  pali  mtima  omwe  uli  odekha  ndikukhazikika  kuposa  mtima  wa  kuwala  kwa  maso  a  Mtumiki(s.a.a.w) amene  ali  bwana  wa  anthu  onse  ofera  mu  njira  ya  Mulungu Husain (a)?
Yemwe  adakumana  ndi  mavuto  akulu  oti  vuto  lina  lililonse  palokha  limakwanira  kugwedeza  phiri  lomwe  laima  molimba,  monga  asilikali  ake  onse,  azibale  ake  ndi  ana  ake  adaphedwa  mwini  wake  akuona  ndi maso  ake.
Onena  nkhaniyi  akuti:  nthawi  ina  iliyonse  yomwe  masiku  amayandikira  ku Ashura ( pa 10 mwezi wa Muharram)  mavuto  amenewa  adali  kukulirakulira  kukhala  ngati  kuti  kukumana  kwake  ndi  Mulungu  wake  ali  odekha  ndi okhazikika  mtima  kudali  kukuyandikira.
Inde,  pali  ma  aya  ambiri  omwe  anena  za  nkhani  ya  Husain,  koma  aya  iyi  yasankhidwa  chifukwa  choti  ndi aya  yomwe  ikuonetsera  kwambiri  za Husain (a)  zakudekha ndi kukhazikika  kwake mtima.
Imam  Swadiq (a)  adanena  kuti: Sura ya  Fajir  muyenera  kuiwerenga  nthawi  yomwe  mukupemphera  mapemphero  okakamizika(wajib)  komanso  osakakamizika( Mustahab)  chifukwa sura  imeneyi ndi  ya Imam  Husain(a)  ndipo  mitima  yanu  imangire  za  sura  imeneyi,  Mulungu  akuchitireni  chisoni  ndikukhululukirani   machimo  anu.
Abu  Usamah  yemwe  adali  nawo pamalo omwe  Imam  Swadiq  amanena  izi  adafunsa  kuti  kodi  ndichifukwa  chiyani  sura  imeneyi  ikukhudzana  ndi  Imam  Husain(a)?  Imam  adati: kodi  iwe  sukumva  mau  achoonadiwa  omwe  akunena  kuti  e!  iwe  mtima  odekha  ndi okhazikika, mauwa  akutanthauza  Imam  Husain(a)  chifukwa  iye  ndi  “nafusil mutumainnah” ndipo  ndiosangalalidwa  ndi  Mulungu. Sura  imeneyi  idatsikira  iye  ndi  omutsatira  ake  ndi  onse  otsatira  akunyumba  kwa  Mtumiki(s.a.a.w) ndipo  munthu  wina  aliyense  yemwe  angawerenge sura imeneyi  mowilikiza   akakhala  ndi  Imam Husain  malo  amodzi  ku mtendere, Mulungu  ndi  wamphamvu komanso  ozindikira china  chilichonse.
Monga  momwe  timakhala  tikunong’oneza  bondo  kuti  kalanga  ine!  ndidakakhala  mugulu  lanu  ndikuphedwa  limodzi  nanu  ndicholinga  choti  nafenso tikhale  opambana  kwakukulu, tiyeni  tiyesetse  kuti  zochita  zathu,  zonena  zathu  zikhale  zofanana ndi  Imam  Husain(a)  kuti  mwina  Mulungu  akakhale  osangalala  nafe  monga  momwe  surayi  ikunenera  chifukwa 
رضوان من الله اكبر ife  tikudziwa  kuti  mphoto ya  chisangalalo  cha  Mulungu  chimenechi  ndi yayikulu  yomwe  ndi  mtendere.
Kuzipereka  komwe  Imam  Husain(a)  adaonetsa  pamodzi  ndi  anthu  ake  kuli  koti  mbuyomu  kudalibe  ndipo sikudzapezeka  angakhale mtsogolo  momwe. Awa  adali mayesero  kwa iye. Chofunika  pankhaniyi ndichakuti  Asilamu  alero  lino ayenera  kutengera  phunziro  pakuzipereka pofuna kuteteza  chipembedzo  ndikulimbana  ndi  anthu  opondereza  ndikuzikweza  monga  momwe tidaonera  asilikali  adziko  la  Iran  polimbana   ndi anthu  omwe  amafuna  kubweretsa  zinthu  zosemphana  ndi  chisilamu,  iwowa  adatengera  phunziro  kwa  Imam  Husain(a) pofera  munjira  ya  Mulungu  ndikukhala  opambana  kwakukulu.
Tipemphe  Mulungu  kuti  mtima  ofuna  kufera  munjira  yake  usatichoke  ndiponso  tikhale  anthu  omvera  akulu akulu  achipembedzo  omwe  ali olungama  (momwe  zilili  ku  Iran  kuti  amamvera  ndikutsatira  mtsogoleri  wamkulu  Khamenei)  kuti  mtsogolo muno  tidzakhale  onyamula  mbendela  ya Imam  wanthawi  yathu  ino  Mahdi (a.f).