Ubwino wa Imam Husain 1

Ubwino wa Imam Husain 1

 

Ubwino  wa  Imam  Husain 1 

Mtumiki  Muhammad(s.a.a.w) adanena  kuti:
إنّ لقتل الحسين - عليه السلام - حرارة فى قلوب المؤمنين لا تبرد أبداً.
(( Kuphedwa  kwa  Imam  Husain (a)  ndi  moto  omwe  wakolezedwa  mmitima  mwa  anthu  okhulupirira  omwe  sudzathimitsidwa mpaka  kalekale)).
Mfunso  lomwe  likufunsidwa pamalopa  ndi loti kuti  Husain  ndi  ndani?
Kodi  Husain  ndi  ndani  oti  kulimbana  kwake  ndi  anthu ofuna  kuononga  chisilamu  kulipo  mpaka  kalekale?
Husain  ndi  ndani  yemwe  magazi  ake  akuzutsa  anthu  pambuyo  pakudutsa   nthawi  yayitali?
Husain  ndi  ndani  yemwe  chiphunzitso  chake  chili  chosula  anthu?
Husain  ndi  ndani  oti  dzina  lake  lili  mkamwakamwa  mwa  zilankhulo  zosiyanasiyana?
Husain  ndi ndani  oti  makhalidwe  onse  abwino  asonkhana  mwa  iye?
Husain  ndi  ndani yemwe  ali   sitima  yachipulumutso  komanso  nyale  yachiongoko?
Husain  ndi  ndani  yemwe  wakhazikitsa  kukonda  kufera  mu njira  ya  Mulungu, kuopa  Mulungu, kuzindikira, chikondi, chifundo  ndi  makhalidwe   abwino  dera  la  Karibala?
Husain  ndi  ndani  yemwe  kuphedwa, kupezeka ndi  kulimba  kwake  kuli  chinthu  chozizwitsa  nthawi  zonse?
Husain  ndi  ndani  yemwe  sadakhale  chete  ndi  kupondereza?
Husain  ndi  ndani  yemwe  mmalo  mogonjera  adasankha   kufera  munjira  ya  Mulungu?
Husain  ndi  ndani  yemwe   adalimbana  ndi  makhalidwe  oipa ndi   onyozeka?
Husain ndi  ndani  yemwe  kulira  pomukumbukira  kuli  ngati  munthu  akubwezeretsa  thupi  lake  mmalo  pambuyo  poti  lidaonongeka?
Husain   ndi  ndani  yemwe  pamanda  pake  ndi  malo  omwe  anthu  amapezera  chichilitso?
Husain  ndi  ndani  yemwe  chikondi  kwa  iye  zili  ngati  kuti  munthu  wateteza  katundu  wake  wapadziko  lapansi  ndi  tsiku  lomaliza?
Husain  ndi  ndani  yemwe   pofuna  kuti  chipembedzo  chipitilire  adalolera  kutsogoza  ana  ake  okondedwa?
Husain  ndi  ndani  yemwe   agogo  ake  olemekezeka  Muhammad(s.a.a.w)  adanena  kuti((  Husain  ndi  ochokera  mwa  ine  ndipo  ine  ndiochokera  mwa iye))?
 Inde,  uyu ndi  Husain  yemwe  Mulungu  adampatsa  dzina  loti 
نفس المطمئنة  (( mtima  odekha  ndikukhazikika)).
Uyu  ndi  Husain  yemwe  dothi  lopezeka  pa  manda  ake  ndi  chichilitso.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  adaphedwa  poitanira kuzinthu  zabwino   ndikuletsa  zinthu  zoipa.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  kuphedwa  kwake  kuli  kwa  pamwamba.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  zolankhula  zake ndi  zopereka  phindu.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  adasankha  imfa  ya ulemerero  mmalo  mwa  imfa  yonyozeka.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  adaphunzitsa  anthu  nkhani  ya kufuna ufulu  ndikulemekezeka   kwa  munthu.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  kumulilira  iye  kumabweretsa  kuwala  mumtima.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  adalimbana  ndi  asilikali  a adani  okwana  30,000  popanda  kugonjera  iwo.
Uyu  ndi  Husain   yemwe  angakale  kuti  ana  ake  adadulidwa-dulidwa   koma sadagonjebe.
Uyu  ndi  Husain  yemwe   adasiya zonse  chifukwa  cha chikondi  kwa  mbuye  wake.
Uyu  ndi  Husain  yemwe  adalikuyamikabe  Mulungu  ndikupirira  angakhale  mwana  wake  wamiyezi  isanu  ndi  umodzi  adabaidwa  ndi  mkondo  wansonga  zitatu.
Uyu ndi  Husain  yemwe  magazi  ake  adali  mmalupanga a adani  komabe  kupambana  ndikwake.
Husain  ndi  tsogoleri  yemwe  amakondedwa  ndi  Atumiki    onse  ndipo  amakhala  akumulilira.
Uyu   ndi  Husain  yemwe  pambuyo  pakuphedwa kwake  utsogoleri  opanda  pake  wa  mabani  umayyah  udazindikira  kuti kulimba  kwake  atamwalira  kuli  koposa  nthawi  yomwe  adali  moyo.
Tiyeni  ifenso  titengere  phunziro  kuchokera  kwa  Husain (a)  pokhala  olimbana  ndi  adani  achisilamu    kuzipereka, mphamvu, kukonda  chipembedzo,kufuna  ufulu,kupirira,kulamulira  zinthu  zabwino ndikuletsa  zinthu  zoipa ndi kufuna  kufera  munjira  ya  Mulungu, ndipo  ngati  tingathe  kukwanitsa  kupanga  izi  titha  kunena  kuti  ife  tili  limodzi  ndi  Husain(a).
Akulu akulu  omwe  adamvetsetsa  nkhani  imeneyi  ya  Husain  amailongosola  mwachikoka  ndimopereka  chidwi  motero  nkhani imeneyi  idzapitilira  mpaka  mitundu  yobwera  mtsogolo adzaipeza.
Mulungu  aipange  imfa  yathu  kukhala  ngati  ya  Husain  pofera  munjira  yake  ndikukhala  yolemekezeka.