Imamah (utsogoleri wa pambuyo pa Mtumiki) mu Quran 1

Imamah (utsogoleri wa pambuyo pa Mtumiki) mu Quran 1

Imamah (utsogoleri wa pambuyo pa Mtumiki) mu Quran1
Suratul Qadr ndi imodzi mwa ma Surah omwe ali apamwamba kwambiri ndipo pali Thawab zambiri kwa munthu yemwe angamvetsetse zomwe Surayi ikunena. Ndi Surah imeneyi titha kutsimikizira kuti mudziko lino muli cholengedwa china chake  cha mtengo wapatali chomwe chaka china chirichonse angelo amakhala akuchitsikira pokhudzana ndi china chirichonse chidzakhala chikuchitika muchakamo.
Muchikhulupiliro chathu (Shia) cholengedwa chimenecho ndiye mtsogoleri wanthawi yathu ino yemwe ali Imam Mahdi (A.A.T.F) ndipo ena palibe chomwe angayankhe pankhaniyi.
Mu Surah imeneyi tikupezamo fundo zingapo.
Fundo yoyamba ndi yoti mudziko lapansi lino muli Khalifa wa Mulungu. Fundo yachiwiri, Khalifayo ali ndi udindo wapamwamba kufikira kuti Wahay ukumutsikira – osati Wahay wa Quran ayi – ndinso chachitatu ndi choti Khalifa wa Mulunguyu amadziwa china chirichonse. Monga amadziwa zomwe ife tikupanga ndinso kwina kulikonse komwe tingakhale. Akudziwa mapeto a umoyo wanga pano padziko lapansi komanso kudziko la Akhira. Zonsezi muchifuniro ndi mphamvu ya Mulungu.
Mulungu wapamwamba akulongosola mu Surah imeneyi kuti:
إنا أنزلناه فی لیلة القدر
“Ndithudi ife tayitsitsa Quran mu Usiku wa Qadr (Usiku wa Mulingo)”
وما أدراک ما لیلة القدر
“Ndichiyani chingakudziwitse iwe za Ulemelero wa Usiku wa Qadr”
لیلة القدر خیر من ألف شهر
“Usiku wa Qadr ndi wabwino kwambiri kuposa miyezi 1000”
Mulungu mu usiku wa Qadr adawapangira chisoni akapolo ake kuti chifukwa cha kuwupeza usiku umenewu, Mulungu adzawalembere ma ubwino oposa miyezi 1000. Kutanthauza kuti mwachitsanzo ngati wapeleka Sadaqah 1 Kwacha ndiye kuti idzakhala ndi maphindu okwana 1000 kwa Mulungu, ngati wapemphera Swala imodzi ndiye kuti Mulungu adzakupangira chisoni kuti pemphero lakolo lidzakhale ndi maphindu okwana 1000.
Tisanapitirize kulongosola kwathuku apanso ndi kwabwino kuti tikumbutsane fundo iyi kuti ngati Mulungu adawutenga usiku wa Qadr kuti ndi wabwino kuposa miyezi 1000, zidanenedwanso m’mahadith kuti ubwino umenewu kuti munthu awupeze, sikuti ungokhala usiku wa Qadr okha basi, itha kukhala nthawi ina posakhala usiku umenewu komanso sikuti mpakana ukhale usiku onse ayi. Ola limodzi kapenanso ayi mphindi zingapo zokha zomwe zingakupangitseni inu kusintha muchikhulupiliro poganiza ndi kutenga njira ya chilungamo. Nthawi yochepa imeneyi idzakhala ndi ma ubwino ofanana ndi usiku wa Qadr.
Ma hadith akutiwuza kuti tipange chiyani kuti tipeze ubwino umenewu? Kuganizatu basi.
تفکر ساعة خیر من عمل سبعین سنة
“Kuganiza mu ola kapena mphindi imodzi yokha ndi zabwino kwambiri kuposa ntchito yomwe munthu angagwire zaka makumi asanu ndi awiri 70”.
Abale anga okondedwa sikuti mpakana uchite kukhala usiku wa Qadr kuti mupeze ubwino ochuluka chonchiwu, ngakhale osakhala nthawi ya usiku wa Qadr, pomwe mulipo tangokhalani muganize mozama, kuganiza kwanu kozama mumphindi zochepazi kudzatha kukhala kwapamwamba ngati ubwino wa usiku wa Qadr. Kuganiza kwanu kozamaku mwina kudzatha kutengapo gawo pa chisangalalo chanu chosatha.
Kutanthauza kuti ine pokhudzana ndi umoyo wanga osatha ndidali ndikupita kuchiwonongeko koma kudutsira mukuganiza kwa nthawi yochepaku ndikomwe kwapangitsa kuti umoyo wanga osatha ulongosoke koma izi zikuchitika munthawi yosakhala ya usiku wa Qadr.
Ndabwera ndikuganiza mozama munthawi yochepa ndipo ndapeza njira yeni yeni yachilungamo mapeto ake ndasintha njira yolowera.
تفکر ساعة خیر من عمل سبعین سنة
Zowonadi Hadith imeneyi ndi imodzi mwa ma Hadith omwe ali odabwitsa kwambiri.
Kuganiza!
Munthawi yochepayi tidzayenera kuganiza kuti kodi tikupita kuti?
Kutanthauza kuti munthu usiku ndi usana adzayenera kuganiza podzifunsa mafunso atatuwa:
Ndachokera kuti? Ndiri kuti? Nanga ndikupita kuti?
Apanso ndipomwe tikuwonanso kuti pali Hadith inanso yodabwitsa kwambiri pankhani imeneyi yomwe ikunena kuti:
رحم الله امرءا علم من أین و فی أین وإلی أین
“Mulungu wamudalitsa munthu amene wazindikira kuti wachokera kuti ndipo ali kuti nanga akupita kuti”.
Chabwino nkhani yathu ndi ya usiku wa Qadr kuti ukuposa miyezi 1000.
Zowonadi mu usiku umenewu m’machitika zinthu zambiri zikulu zikulu. Kodi zinthu zimenezi ndi ziti?
Chinthu choyamba chomwe chikuchitika mu usiku umenewu ndiko  kutsika Quran kuchokera kwa wapamwambayo.
Kodi Quran imeneyi ikutsika bwanji?
تنزل الملائکة و الروح
Kutanthauza kuti Quran ikutsika pamodzi ndi angelo komanso (Ruh). Zidafunsidwa mu hadith kuti kodi Ruh ndi chiyani? Zidayankhidwa kuchokera kwa anthu omwe Mulungu adawasankha kukhala osalakwa mu umoyo wawo onse osachimwa kuti: Ruh ndi mngelo amene ali wamkulu kwambiri kuposa angelo onse.
تنزل الملائکة و الروح فیها بإذن ربهم من کل أمر
“Amatsika angelo ndi Ruh mu usikuwo ndichilamulo chabwana wawo pokhudzana ndi china chirichonse chomwe chidzachitika”.
Kutanthauza china chirichonse chomwe chidzachitika mu chaka chimenechi chimalongosoledwa mu usiku umenewu. Ndiye kuti choyamba chake ndiko kutsika kwa Quran kenako kulongosola china chirichonse chomwe chidzachitike mudziko lino lapansi.
Pali ma Hadith ambiri omwe adanena za ubwino owerenga Surah imeneyi. Akulu akulu Surah imeneyi ndi yodabwitsa kwambiri. Imodzi mwa Swala zomwe zidanenedwa kuti ndi bwino munthu atapemphera ndiyo Swala ya Mtumiki. Swala ya Mtumiki kutanthauza kuti ndi pemphero lomwe likukuwandikitsa iwe ndi Mtumiki. Kodi mu Swala ya Mtumiki mumayenera kutani? Mukakhalidwe kena kalikonse muyenera kuwerenga Quran. Ndi Swalat yodabwitsa kwambiri.
Muli chiyimire muyenera kuwerenga  Surat Qadr kokwana khumi ndi kasanu 15, mukawelama pambuyo powerenge Dhikr ya Ruku muyenera kuwerenga Surat Qadr kokwana 15. Mukawelamuka werengani Surat Qadr kokwana 15, mukapita mu Sajdah werengani Surat Qadr kokwana 15. Imeneyi ndi Swala yodabwitsa kwambiri imene mukakhalidwe kena kalikonse munthu akuwerenga Quran. Kutanthauza kuti munthu ndi Swala imeneyi akutenga mphamvu kuchokera kwa Mulungu kapenanso mukulongosola komveka bwino tinganene kuti munthu akulowera kumalo apamwamba.
Chifukwa chakuti panthawi yomwe munthu akuwerenga Quran ndiye kuti akupita kumwamba (Miiraj) ndipo Quran ikukupeputsa iwe kupita kumwamba ndipo ukapita m’mwamba udzafika malo owandikira kwambiri ndi Mulungu yemwe ali Mtumiki chifukwa chinthu chomwe chiri chowandikira kwambiri ndi Mulungu ndi Mtumiki wathu okondedwa Muhammad (S.A.A.W).
Zowonadi Mtumiki wathu ndi amene adakwanitsa kufika pafupi ndi Mulungu pomwe Quran ikunena kuti:
فکان قاب قوسین أو أدنی
“Adawandikirana ndi Mulungu mlingo wa kugenda kwa Uta kuwiri kapena adawandikira koposera apo”
Surah imeneyi ndi yodabwitsa kwambiri powona kuti ikuwerengedwanso mu pemphero la Mtumiki.