Kukambirana pakati pa chikhirisitu ndi chisilamu 3

Olemekezeka Yesu (mtendere wa Mulungu ukhale kwa iye) ndi mzimu wa Mulungu, liwu la Mulungu komanso ndi mtumiki wa Mulungu, adabadwa popanda bambo, adalankhula ali khanda, adali kudzutsa akufa, kuchiza matenda akhate, kuwaonetsa akhungu, adali kupereka moyo kuchinthu chowumba, kulankhula zobisika ndi zina zotero. Munthu osakhulupilira zimenezi ndiye kuti simsilamu ayi. Koma zonsezi sizikutanthauza kuti iye ndi Mulungu kapena mwana wa Mulungu. Kubadwa popanda bambo sichifukwa kuti iye akhale Mulungu kapena mwana wa Mulungu.

AttachmentSize
File 3dccf63164fcde0f4f23589c7fa2ac04.mp430.25 MB