Kulankhula kwa kholingo lodulidwa – Imam Husein (a.s) part 1

Ee inu onditsara ine! Nthawi zonse mukamamwa madzi ndikumbukireni ine. Mukamva zakuphedwa kwa munthu, ndikumbukireni ine. Ine ndi mwana wa mtumiki (mdzukulu) yemwe ndidaphedwa popanda tchimo. Ateketa ndi kulipondaponda thupi langa ndi ma Hatchi akulu akulu pambuyo pondipha. Mukadakhalapo (inu asilamu) patsiku la Ashura ndikumandiwona ine zomwe zimandichitikira. Adakana kundimvera chisoni pomwe ndidali kumupemphera madzi mwana wa miyezi 6 ndipo m'malo mwake adamuyankha mwanayu ndi mkondo omwe udazinga khosi lake. Anthuwa adavulaza mtima wa mtumiki (S.A.A.W).

AttachmentSize
File 1c4a99ec9d5c7b03912f5d85cb06ea7e.mp421.85 MB