Zolankhula za Imam Baqir (a.s)2

Imam Baqir (a.s) adanena kuti: عالمٌ يُنتفع بعلمه أفضل من سبعين الفَ عابدٍ - Munthu yemwe wagwira ntchito yayikulu pophunzira ndikuthandizika iye mwini komanso anthu ena powawunikira njira yachoona, munthu otereyu ali wabwino kuposa akapolo a Mulungu okwana chikhwi chimodzi. - Munthu amene akupembedza Mulungu ndikumulambira ngati angachite zimenezi mwachoonadi ndiye kuti azipulumutsa yekha, pomwe munthu amene ali ophunzira akalalikira kwa anthu kapena kulemba bukhu adzathandiza anthu ambiri kudzera mu ntchito imeneyi. - Munthu ophunzira ali ngati miyala yolimba yomwe imapangidwira foundation ya nyumba yomwe imapangitsa kuti nyumba ilimbe, iwo chifukwa cha chiphunzitso chomwe amakhala nacho muchipembedzo, zimapereka chilimbikitso kwa anthu. - Ndilankhulepo kwa anthu omwe ali ndichizolowezi choti akamuwona munthu ophunzira kapena munthu yemwe wabwera pa sukulu yophunzirira amamunyoza, adziwe kuti anthu amene mukuwanyozawa akusungidwa ndi Mulungu ndiye musamaleni Mulungu, chifukwa munthu ameneyu wabwera kuti amudziwe Mulungu, adziwe zolankhula za Mtumiki kenako akawawuze anthu ena. - Chenjezonso kwa anthu ophunzira kuti asaphunzire ndicholinga choti anthu adzamuyamikire kapena adzapeze udindo wawukulu, koma ayenera kuphunzira chifukwa cha Mulungu. - Nkhaninso ikuti munthu ophunzira ayenera kukhala opirira.

AttachmentSize
File d8011475f9f44791695dc63ca3acba7b.mp413.27 MB

Add new comment