Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 5.

Imam Baqir (a.s) akunena kuti: من لم یجعل اللهُ له من نفسه واعِظاً، فإنّ مَواعِظَ النّاس لن تُغنيَ عنه شيئاً. - Munthu yemwe samazimvera chisoni mwini wake ndiye kuti kumva chisoni kwa anthu ena kulibe phindu kwa iye. Munthu yemwe samazilangiza mwini wake ndiye kuti kulangiza kwa anthu ena kulibe phindu kwa iye. - Munthu amafunikira kuti akhale ozilangiza yekha, amvere malangizo kuchokera kwa anthu ena. Munthu yemwe akufuna kulangiza munthu wina safunikira kumulangiza pagulu, chifukwa izi zitha kupangitsa kuti munthu apse mtima zomwe mapeto ake ndikulankhula zoipa kwa iwe, kapena sangamvere malangizo ako.Palinso mau oti kulangiza munthu pagulu kumapangitsa kuti munthu olangiza agwe mmavuto akunyozedwa ndi zina. Tipemphe Mulungu kuti atipange kukhala anthu ozilangiza tokha asanatilangize wina.

AttachmentSize
File 4e4654380465274df93690137096549e.mp416.37 MB

Add new comment