Zolankhula za Imam Baqir (a.s) 1.

Imam Ridha (a.s) adanena kuti: قال الامام الرضا (ع): قإِنَّ النَّاسَ لَوْ عَلِمُوا مَحَاسِنَ‏ كَلَامِنَا لَاتَّبَعُونَا ((Zidakakhala kuti anthu adadziwa ubwino, chiphunzitso ndi maphunziro omwe akupezeka mu zolankhula zathu ife akunyumba ya Mtumiki (s.a.w.w) adakatitsatira)). Zili choncho chifukwa choti mkati mwa mau a Ahlubait (a.s) muli: - kumuphunzitsa munthu kuganiza molondola. - kuphunzitsa anthu kukhala umoyo wolongosoka. -kukhutura zinthu zomwe zili zobisika kwa munthuyo zomwe zili zothandiza moyo wake. Imamuyu akuti: الكمال كلّ الكمال التفقّه في الدين Mapeto akukwanira kwa munthu ndiko: - kuzama muchipembedzo. - kuganiza pankhani ya chipembedzo. - kuchita kafuku fuku muchipembedzo. Mapeto antchito imeneyi ndioti: munthu adzadziwa chipembedzo chake. Chitsanzo: Munthu atati wakagula fridge ndikupatsidwa kabukhu komwe mkati mwake muli ndondomeko yosamalira kapena kugwiritsira ntchito fridgeyi, ngati munthu sangagwiritse ntchito ndondomeko imeneyi kapena kabukhuka sadapatsidwe ndiye kuti moyo wa fridge imeneyi udzakhala wawufupi. Mulungu adatilenga ife ndikutiyika pano padziko lapansi ndipo munthu pano padziko lapansi amabadwa kamodzi ndiponso amamwalira ndikuchoka pano padziko kamodzi. Mulungu pofuna kutifotokozera zinthu zoyenera kutsatira kuti kodi pano padziko lapansi tizikhala bwanji, tiziganiza bwanji ndi zina adatitumizira chipembedzo. - Imam Baqir (a.s) akunena kuti: Munthu kuti akhale okwanira ayenera kuchidziwa chipembedzo. -Mtumiki olemekezeka akunena kuti: إِذَا أَرَادَ اللَّهُ‏ بِعَبْدٍ خَيْراً فَقَّهَهُ فِي الدِّينِ. ((Mulungu akafuna kupereka zinthu zabwino kwa kapolo wake amamupanga kukhala odziwa ndikuzindikira chipembedzo)). Inu lero lino mukawona dziko lino lapansi muona kuti pali zinthu zambiri zomwe anthu akuchita pofuna kusocheletsa anthu ena monga kukhazikitsa ma tv station osakhala bwino, kuyika zinthu zosakhala bwino pa internet ndi zina, ndiye ngati munthu sangadziwe chipembedzo chake bwino ndiye kuti asocheletsedwa ndi anthu amenewa. Pali ma tv station ambiri kapena ma wailesi kapena ma bukhu ambiri omwe amawoneka ngati akuphunzitsa zinthu zabwino koma chonsecho akuyitanira ku zinthu zoipa. Tsono pachifukwa ichi munthu ayenera kudziwa chipembedzo kuti azindikire kuti chikuti chiyani nanganso anthu amenewa akuti chiyani, ndiye Imam Baqir (a.s) akunena kuti munthu akafuna kuti akhale okwanira kweni kweni ayenera kuchidziwa chipembedzo chake bwino. Komanso akuti: - الصّبرُ على النّائبَة -Munthu ayenera kupirira kumavuto omwe akukumana nawo mu umoyo wake, zoona zake ndizoti munthu aliosakanikirana ndi mavuto, tisayiwalenso kuti munthu mmene angakhalire okhulupirira mavutonso amakhala chimodzimodzi. Mulungu akunena mu Quran yake yolemekezeka kuti: (( وَ لَنَبْلُوَنَّكُمْ بِشَيْ‏ءٍ مِنَ الْخَوْفِ وَ الْجُوعِ وَ نَقْصٍ مِنَ الْأَمْوالِ وَ الْأَنْفُسِ وَ الثَّمَراتِ وَ بَشِّرِ الصَّابِرِينَ الَّذِينَ إِذا أَصابَتْهُمْ مُصِيبَةٌ قالُوا إِنَّا لِلَّهِ وَ إِنَّا إِلَيْهِ راجِعُون أُولئِكَ عَلَيْهِمْ صَلَواتٌ مِنْ رَبِّهِمْ وَ رَحْمَةٌ وَ أُولئِكَ هُمُ الْمُهْتَدُون )). البقرة: 155- 157 Mulungu akutipatsa mayesero amantha monga momwe zikukhalira maiko ena monga Syria, Afghanistan, Iraq, Lebanon, Pakistan ndi ena. Komanso njala, kuchepekedwa kwa chuma zomwe ndi umphawi, kumwalira kwa okondeka athu, anthu amene paumoyo wathu tidali kwakonda kwambiri monga bambo, mayi, mkazi, mwana komanso kuchepa kwa zokolora. Kuchoka pamayesero onsewa Mulungu akutchula chinthu chomwe munthu ayenera kuchita pambuyo pakukumana ndi mayesero amenewa chomwe ndi kupirira. Chifukwa munthu ukapirira kumavutowa ndiye kuti wasiya nkhani yonse mwa Mulungu mwini yemwe ali odziwa zinthu zonse, komanso munthu mapeto azimenezi ndiye kuti amakumbikira imfa ndipo kudzera mu kukumbukira imfa kumamupangitsa munthu kupulumuka kuchokera ku mavuto ambiri. Munthu akapirira kuchokera kumavuto amapulumuka ndikupeza mtendere utatu uwu: أُولئِكَ عَلَيْهِمْ صَلَواتٌ مِنْ رَبِّهِمْ وَ رَحْمَةٌ وَ أُولئِكَ هُمُ الْمُهْتَدُون 1- amapeza mtendere kuchokera kwa Mulungu wawo. 2-amakhala muchifundo ndi mtendere wa Mulungu. 3- amapeza chiwongoko kuchokera kwa Mulungu wawo. -Imamunso akunena kuti: وتقديرُ المَعِيشة Komanso munthu ayenera kugwiritsa ntchito ndalama zake molingana ndi mmene amapezera. Munthu ayenera kugula zinthu molingana ndi mmene amapezera ndalama. Asafune kugula zinthu zoposa ndalama zomwe amapeza, asakhale ndichiyembekezo chopeza zinthu zoposa ndalama zomwe ali nazo. Munthu akasemphana ndi zinthu zimenezi mapeto ake: - sagona mwamtendere. - amakhala ndi ngongole zambiri. Munthu akakhala ndi ngongole zambiri umoyo wake umafupika. Munthu asakhale odandaula pokhala ndi zinthu molingana ndi mmene amapezera ndalama. Munthu ayenera kuzikhonza yekha ndikukhala okhutitsidwa ndi zinthu zomwe alinazo. Pomaliza tinene kuti zinthu zitatu zimampangitsa munthu kukhala okwanira mu umoyo wake: 1- kuchidziwa ndikuzindikira chipembedzo. 2- Kupirira pamavuto omwe wakumana nawo. 3- Kukhutitsidwa ndi zinthu zomwe alinazo ndikugwiritsa bwino ntchito zomwe alinazo. Mulungu wamphamvu zonse azikuyang\'anirani komanso akudalitseni. Wasalam alikum warahmatullah t

AttachmentSize
File f7244978860f8d75dd8342fe1e9a1875.mp424.79 MB

Add new comment