University yachisilamu yoyamba ku Malawi

University yachisilamu yoyamba ku Malawi

 Pofuna  kulimbana  ndi  vuto  lakusowekera  maphunziro  achisilamu,  dziko la  Malawi  likufuna  kutsekula  University  kuti  achinyamata  achisilamu  akhale  ndi  mwayi  okaphunzira   maphunziro  achisilamu. Polankhula  pamsonkhano  omwe  adakumana  akulu  akulu  a chisilamu, nduna  yoyang’anira  za paulendo  ndi  ntchito  zapagulu olemekezeka  a Sidik  Mia  adati:  tili  ndi  cholinga  chimodzi  pofuna  kukweza  maphunziro  adziko  lino  la  Malawi  choncho  nkhani  imeneyi  ndiyotheka  kudzera  mu  ulamuliro  wabwino.
Iye  adati  ntchito  imeneyi  ichitika  ndichithandizo  chochokera  ku  bungwe  la  Direct AID Society  laku  Kuwait. Monga  momwe  tikudziwira  kuti  pali  mauniversity  angapo  omwe  akhazikitsidwa  muno  m’Malawi  ndi  anzathu  achikirisitu  monga   African Bible College, Livingstonia University  omwe  ali  mmanja  mwa  Church of Central Africa Presbytery, Seventh Day Adventist University  ndi  Catholic University.  Kuonjezera  apa  tilinso  ndi  mauniversity  aboma  atatu. Kutsekulidwa kwa university imeneyi kudzachepetsa  vuto la  maphunziro  mdziko  muno. Ndunayi  idalimbikitsa  asilamu  kuti ayenera  kuzindikira  kufunikira  kothandiza  kukwera  kwa  maphunziro  mdziko  komanso  ndi  anthu  osowa  chithandizo  cha  maphunziro. Ndunayi  idapereka  ndalama  zokwana  k2.5  million  zoti  amangire   mabuloko  ena  asukulu  ya derali ( sub mosque) m’boma  la  Mangochi. Komanso  idapereka  ndalama  zoti  zimangidwire  mizikiti  pa Mathanjesi mu nzinda  omwewu  wa  Mangochi.
Chisilamu  ndi  chipembedzo  chachiwiri  kumwera  kwa  Africa  pambuyo  pa  Chikirisitu.
Tiyeni  asilamu  tiikire  chidwi  pa maphunziro  achipembedzo  chathu.

 

Add new comment