Choonadi cha banja mu Chisilamu
Choonadi cha banja mu Chisilamu
Kodi choona cheni cheni cha banja muchisilamu ndi chiti?
Komanso ndichifukwa chani chisilamu chimalimbikitsa nkhani ya banja?
Sheikh Allamah Muhammad Taqi Ja’afari pofuna kuyankha funso lomwe mkulu wina yemwe ndi Philosopher waku Europe adamufunsa kuti kodi ndichifukwa chiyani chisilamu chimalimbikitsa banja? Adati: “ banja ndi njira imodzi yomwe mtundu wa anthu umapitilira”.
Mu banja mumapezeka zinthu zabwino zambiri monga izi:
1. Chikwaniritso.
Munthu wina aliyense ndioperewera choncho amakhala akutaka-taka cholinga choti athe kupeza chinthu chomwe chimukwaniritse. Mnyamata amakhala akufunafuna mpata oti athe kukhala oziimira yekha pamaganizo ndikuthetsa mavuto ambiri omwe amakhala nawo, pachifukwa ichi amakhala akufunafuna mkazi oyenera kuti athe kumanga naye banja ndikumakhala. Kudzera mubanja limeneli iye amapeza chikwaniritso chomwe amachisowekera nthawi yomwe adali yekha.
Sheikh Mutwahari panganiyi adanena kuti:
Kukhala ndibanja ndichifuniro cha tsogolo la ena chifukwa kuchokera mubanja limeneli anthu ena amapeza chisamaliro ndi tsogolo labwino , ichi chitha kukhala chimodzi mwa zifukwa zomwe chisilamu chimalimbikitsira banja. Mu banja ndi momwe munthu amapeza umunthu wake. Mu banja munthu amakumana ndi zinthu zomwe zimampangitsa kuti akhale okwanira. Munthu amakhala ndikutha kokhala umoyo wapagulu (society).
2. Mpumulo.
Chinthu chomwe chili chofunikira kwambiri m’banja ndi nkhani ya mpumulo chomwe ndi chinthu chomwe chili mu chilengedwe cha munthu pomwe Mulungu akunena kuti:
«وَ مِنْ آياتِهِ أَنْ خَلَقَ لَكُمْ مِنْ أَنْفُسِكُمْ أَزْواجاً لِتَسْكُنُوا إِلَيْها وَجَعَلَ بَيْنَكُمْ مَوَدَّةً وَرَحْمَةً إِنَّ فِي ذلِكَ لآَياتٍ لِقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ(روم/21):
((China mwa zionetsero zake ndikuti adalenga akazi kuchokera mwa inu nokha ndicholinga choti muzipezeramo mpumulo ndipo Mulungu adaika mkati mwakemo chikondi ndi chisoni, mu zinthu izi muli zionetsero kwa anthu omwe ali oganiza)).
Mu ayayi tamva kuti mkazi ndinjira yomwe mwamuna amapezera mpumulo. Nthawi yomwe munthu amakhala wachinyamata amakhala kuti alibe munthu ocheza ndikusewera naye koma akakwatira amakhala kuti tsopano ali ndi omuchotsa kusungulumwa, inde banja ndi mtendere ochokera kwa Mulungu. Anthu omwe ali odziwa nkhani za science ndi humanity adavomereza kuti kukumana malo amodzi kwa mwamuna ndi mkazi kumabweretsa mtendere ndi kuyenda bwino kwa nzeru mthupi la munthu, ndipo kupanda kutero kumabweretsa vuto mthupi ndi nzeru za munthu.
3. Kupitiliza mtundu.
Ubwino wina wa Banja oti ana akabadwa ana amenewa amapitiliza mtundu wa anthu zomwe zili zinthu zofunikira pa dziko lapansi. Nkhani yopitiliza mtundu imeneyi sifunikira kuitenga ngati nkhani yopanda pake monga momwe anthu amaganizira posaikira mtima pa banja ndikumapanga zinthu zosalongosoka zomwe mapeto ake zitha kuthetsa mtundu, chifukwa cholinga chopangira ndiye kuti mtundu upitilire kuti anthu apezekemo. Banja likakhala labwino ndiye kuti limatulutsa ana abwino omwe amakhala opembedza, angwiro,oyera mtima ndi ogwira ntchito zabwino, izi ndizinthu zomwe Mulungu akuzifuna kuchokera kwa anthu.Mukuona kwa Chisilamu banja likakhala ndi mwana wabwino ndi wangwiro zimatengedwa kuti makolo awiri amwanayu agwira ntchito yoyera ndi yabwino, ndipo mwana ameneyu adzakhala ofunikira padziko lapansi nditsiku lomaliza.
Mtumiki(s.a.a.w) polimbikitsa nkhaniyi adati: (( Kodi pali vuto lanji kuti munthu okhulupirira akwatire mkazi kutheka Mulungu kudzera mwa mkazi ameneyu adzampatsa iye mwana wabwino yemwe ndikulankhula kwake mau oti ((Palibe wina omupembedza muchoonadi koma Mulungu mmodzi yekha)) angagwedeze dziko.
Banja limapangitsa kuti munthu akhale mwaufulu ndi mopanda mantha.
Banja ndi kampani yopititsira patsogolo mtundu wa anthu.
Banja ndi pothawira ndi pobisala pa mwamuna ndi mkazi.
Banja ndi limapangitsa munthu kuti cholinga chokhalira pagulu achimvetsetse.
Banja limapangitsa kuti umoyo wapagulu ulimbikitsidwe.
Banja limapangitsa kuti vuto lomwe adali nalo lofuna mkazi lithetsedwe mokwanira.
Banja limateteza munthu kuchokera kumatenda a pa thupi ndi mmutu.
Banja limateteza munthu kuchokera kuzochitika zotailira monga chigololo ndi zina.
Pomaliza ndipemphe Asilamu onse kuti alitenge banja kukhala chinthu chofunikira kwambiri muchipembedzo chathu cha Chisilamu. Amene sadakwatire ndibwino kuti akwatire Mulungu amudalitsa, amene adakwatira ayenera kulemekeza banja lake ndikukondana pakati pawo kuti ubwino wa banja upezeke.
Wassalam alaikum warahamatullah ta’ala wa barakatuh.
Add new comment