Ziyaratu Ashura 2

Ziyaratu  Ashura 2
Pali  anthu  ena  amanena  kuti   palibe  kufunikira  kofufuza  nkhani  yomwe  idachitikira   kale  ndipo  idatha,  kulankhula  kotero  ndikosavomerezeka  chifukwa  chonena  kuti  angakhale  anthu  opanda  chipembedzo  amakhala  akusunga  ndikumakumbukira  zinthu  zakale  kusonyeza  kufunikira  kwa  izo, tsono  ife  Asilamu  tisakumbukire  bwanji  mavuto  omwe adatigwera  muchipembedzomu.
Anthu  amaganizo  amenewa   ndiye  kuti   amatsutsananso  ndi  Ziyaratu  Ashura  imeneyi, koma  anthu  oterewa  Mulungu akuwatenga  kuti  ndi okanira  pomwe  akunena  kuti:
((يا  أيّها الذين  أمنوا لا تتولّوا  قوماً  غضب  الله عليهم  قد  يئسوا  من  الآخرة  كما  يئس  الكفّار  من  اصحاب القبور))
  ((E! inu  anthu  amene  mwakhulupirira,  musawatenge  anthu  omwe  Mulungu  adawakwiira  kukhala  anzanu  chifukwa  anthu  amenewa   adataya  mtima  za  nkhani  ya tsiku lomaliza  chifukwa  cha ntchito  zawo  zoipa  monga  momwe  adataira mtima   anthu  okanira   omwe  adaikidwa  mmanda)).
Pachifukwa  choti  anthuwa  ali okanira  za  Mulungu  ndiye    Mulungu  akuwachotsa  mu gulu  la  anthu  ake okondedwa  mukulankhula   kwake    mu  Quran  kuti:
(( و لا تصلّ  على احد  منهم  مات  ابداً  ولا تقم  على  قبره  انهم  كفروا  بالله  و رسوله  و ماتوا وهم  فاسقون ))
)) Usawapemphere  iwo   akafa   ndipo  usaime pa manda  awo  chifukwa  choti  adakanira  Mulungu  ndi  Mtumiki  wake  mpaka  adamwalira  adakali  anthu  owononga)).
Abale  olemekezeka   Ziyarat  imeneyi  imamupangitsa  munthu  kuti  athe  kumuzindikira  Imam  wake  monga  momwe  zilili  zofunikira  kutero   chifukwa  Mulungu  adasonkhanitsa  zinthu  zonse  zomwe  zikukhudzana  ndi  umoyo  wa munthu  pambuyo  pa  Mtumiki(s.a.a.w)  kwa Imam  monga  momwe  akunenera  kuti:
((وكلّ شيء  احصيناه  فى  امام  مبين ))  (( Zinthu  zonse  tazisonkhanitsa  mwa  Imam  wachionekere)).  Apa  akufuna  kutiunikira  kuti  Msilamu wina  aliyense  ayenera kukhala  ndi  Imam (tsogoleri)  wa nthawi  yake  yemwe  akhale  akuthetsa  mavuto  ake.
Idalandiridwa  nkhani  mu bukhu  la   Uyun  ndi  Amali  Swaduq  kuchokera kwa  Rayan  Shabib , iye  adanena  kuti :  tsiku  loyamba  la  mwezi  wa  Muharram  ndidapita  kwa  Imam  Ridtha  (a), Imamuyu  adati  kwa  ine: kodi  iwe  mwana  wa  Shabib  ukusala?  Ndidati  ayi,  kenako  Imam  adayamba  kulongosola   nkhani  ya  mwezi  umenewu  wa  Muharram  ndi  mavuto  omwe  adagwa   mumweziwu  omwe  ndi    kuphedwa  kwa  Imam  Husain (a),  mukulankhula  kwake  adali  kunena  kuti: e!  iwe  mwana  wa  Shabib,  mwezi  uno  wa  Muharram   ndimwezi  omwe  anthu  anthawi  ya  umbuli  adali  kuletsa  kupondereza  ndi  kumenya  nkhondo  chifukwa  cha  kulemekezeka  kwake  koma    gulu la  asilamu  ili  silidathe  kuzindikira  ulemelero  wa  mweziwu  ndi  ulemeleronso  wa Mtumiki (s.a.a.w)   motero  iwo  adapha  chidzukulu  cha  Mtumikiyu   mmwezi  umenewu  wa  Muharram,  kuzunza  ndikuvutitsa  azimayi  omwe  adali  nawo  ndipo  adatenga   chuma  chawo,  Mulungu  sadzawakhululukira  iwo   angakhale  pang’ono.
E!  iwe  mwana  wa  Shabib  ukafunira  kulira  chifukwa  cha  chinthu   china  chake  uyenera  kumulilira  Imam  Husain (a)   chifukwa  adamupha  ngati  momwe  amaphera  nkhosa. Adaphanso  amuna  okwana  18  (omwe  ndi  abale  ake)  omwe  adalibe   ofanana  nawo.
Nthawi  yomwe  anthuwa  amaphedwa   kumwamba  ndi pansi  pano  padali  kuwalilira,   angelo  okwana   zikhwi  zinayi  adatumizidwa  kudzaikira  umboni  za  kuphedwa  kwawo  ndipo  atafika  adawapeza  kuti  ndithu  aphedwadi,  pachifukwachi  iwo  adalamulidwa  kuti aime  pa manda  a Imam Husain  adakali  ndifumbi  mpaka  tsiku  lomaliza  ndipo  iwo adzakhala  omuthandiza  iye  ndikumalankhula  mau  oti  “ya  latharatil  Husain”.
E!  mwana  wa  Shabib,  bambo  anga  adanena  mau  omwe  adawamva  kwa  bambo  awo  nawonso adamva  kwa  agogo  awo  kuti:  Agogo  anga  Husain (a)  ataphedwa  kumwamba  ndi  dothi  zidasanduka  zofiira , e!  mwana  wa  Shabib  ngati  ungalire  kumulilira  Husain  mpaka  misonzi  kutsikira  mmasaya  ako  dziwa  kuti  machimo  onse  omwe  udawapanga  akulu  kapena   ang’ono   ambiri  kapena  ochepa  adzakhululukidwa. 
E!  mwana  wa  Shabib, ngati  ukufuna  kuti   udzakumane  ndi  Mulungu  ulibe  machimo  uyenera  kumuyendera  Imam  Husain (a) pa manda  ake,  e!  mwana   wa  Shabib,  ngati  ukufuna  kuti  udzakhale  limodzi  mu nyumba  yomwe  Mtumiki  adzakhale  utemberere   anthu  omwe  adapha  Husain(a).
E! mwana  wa  Shabib,  ngati  ukufuna  kuti  udzapeze  zabwino  mofanana  ndi  momwe  adapezera  anthu  omwe  adaphedwa  limodzi  ndi  Husain(a),  uyenera  kunena  mau  awa ((ya  laitani  kuntu  mahumu  fa afuzu  fauzani  a dthima)) 
  ((يا ليتني كنت معهم  فافوز فوزاً  عظيماً))(( kalanga  ine!  ndidakakhala limodzi  nawo  bwezi  nditapambana  kwakukulu))
E!  mwana  wa  Shabib,  ngati  ukufuna  kuti  udzakhale  nafe  pamalo  apamwamba  ku mtendere khala  odandaula  nthawi  yomwe  ife  tili  odandaula,  khala  osangalala  nthawi  yomwe  ife  tili  osangalala  ndipo uyenera  kutsatira  ife  ndikutikonda  chifukwa  choti  munthu  angakhale  ataukonda  mwala  adzadzukitsidwa  nawo  tsiku lomaliza.

 

اشتراک گذاری: 

Add new comment

Fill in the blank.