Ziyaratu Ashura 1

Ziyaratu Ashura 1

MUDZINA  LA  MULUNGU MWINI  CHIFUNDO  NDI CHISONI  CHA  MUYAYA
Inde,  adabweretsa   zida, miyala  ndi  mikondo  kuchokera  ku  nzinda  wa Kufa,
Adabweretsa  udani  omwe  udabindikira  mmitima  mwawo  kuchokera  tsiku la  Ghadir,
Ataona  kuti   munthu  ali  yekha   ndi  dziko  lakutali  adamuthira  nkhondo  ndikumumenya,
Ataona  kuti  munthu   ndi mlendo  adamubweretsera  mavuto  ndi  mazunzo.

M’bale  olemekezeka   usadabwe  ndimmene  kulankhula  kwa mmwambaku  kulili  nkhani  yake  ndi ya  Imam  Husain (a)  yemwe  ndi  mwana  wa  Ali(a)  ndi  Fatwimah (a) chomwe  ndi  chidzukulu  cha  Bwana  wa  Atumiki  onse  omwe  adatumizidwa   Muhammad (s.a.a.w).
Ndikulankhula  kokhaku  kukukwanira  kwa  munthu  kuti  adziwe  kuti  kodi  Husain(a)  adali  ndani  komanso  adali   otani,   umoyo  wake  udali  otani.  Tisaiwale  kuti  Husain  ndi  munthu  yemwe  adasangalatsidwa  ndi  mwini  wake  Mtumiki  kuti  ndi mmodzi  mwa  mabwana  achinyamata  aku  Jannah.  Mauwa  palibe  amene  angawakanire, tsono  funso  ndiloti  kodi  munthu  yemwe   walonjezedwa  kukalowa  ku Jannah  ndi  wabwino  ndiowopa  Mulungu  kapena  oipa?
Tsono  zikutheka  bwanji  kuti  munthu  otereyu   akuphedwa  moponderezedwa  ndimomvetsa  chisoni  chonchi?  Kodi  amene  adamupha  Husain  yemwe  ndi  Yazid   mwana  wa  Muawiyah  ndi wabwino  kuposa  Husain  olonjezedwa  ndi  agogo  ake  Mtumiki  kuti  akalowa  ku Jannah? Kodi  zingatheke  kuti   magulu  awiri  kukhala  pachilungamo  ndikuukirana  kufika  pomenyana  posakhala  kuti  gulu  limodzi  limakhala  pachilungamo  pomwe  limodzi  limakhala  losochera?  Kapena  inu  muli  ndikulankhula  kwina  koposa  zomwe  zanenedwazi?  Ngatidi  muli  munthu ofuna  chilungamo  nkhani  ndiyachionekere  kuti   chilungamo  chidali  ndi  munthu  wakuti,  sichoncho?

Nkhani  yomwe  tikufuna  kuti tikumbutsane  pano  ndiyokhudzana  ndi  Ziyarat  ya  Imam  Husain (a)   monga  ife  maShia  ukafika  mwezi  umenewu  wa  Muharram  timakumbukira  mavuto  omwe  adagwera  ku nyumba  ya  Mtumiki(s.a.a.w)  komanso  Asilamu  onse  dziko  lapansi  yomwe  ndikuphedwa  kopondereza  ndikopanda  chisoni  kwa  chidzukulu  cha  Mtumiki(s.a.a.w)  Husain(a).
Tikamati  ziyarat  timatanthauza  kumuyendera  munthu  wina  wake  kukamuona,  tsopano  ife  mumwezi  umenewu  timakhala  ndi  ntchito  yomuyendera  Husain(a). Ena amapita  ku Iraq  dera lotchedwa Karibala   malo  omwe  adaphedwera  ndikuikidwa  mmanda. Ena  chifukwa  choti  sangathe  kupita  amakwaniritsidwa  ndikuwerenga  dua  yomwe  imatchedwa  Ziyaratu  Ashura.
Ubwino  wa  Ziyarat  imeneyi  ndi:
1. kupeza  chichilitso  kuchokera  mwa iyo. Ngati  munthu angakhale  ndi vuto  la nthenda  ina  yake  akawerenga  dua  imeneyi  Mulungu  amatha  kumuchiza.
2. Mavuto  ndi zovuta  zimachotsedwa  kwa munthu.  Ziyarat  imeneyi  imawerengedwa  ndi  Asilamu  ambiri angakhale  ndi  Ahlu sunnah  wal jamaa  omwe.
3. Anthu   adzazindikira  choonadi  cha  Chisilamu  chifukwa  Husain(a)  adaphunzira  Chisilamu  kuchokera  kwa  bambo  ndi  agogo  ake.  Phunzitsi  wa  bambo ake  ndi  Mtumiki(s.a.a.w),  phunzitsi  wa mai  ake  ndi  Mtumiki (s.a.a.w) ,iye  mwini   phuzintsi  wake  ndi  Mtumiki(s.a.a.w), kusonyeza  kuti   maphunziro  omwe  Husain(a)  adali nawo  amachokera  kwa  Mtumiki (s.a.a.w).Kodi  ndi  ndani yemwe  angachidziwe  chisilamu  kuposa  anthu amenewa?

Chinthu  chomwe  tiyenera  kudziwa  pa  nkhaniyi  ndichoti  kupanda kuti  Imam  Husain(a)   adaima  ndikulimbana  ndi  Yazid bin Muawiyah,  ndiye  kuti chisilamu  chidakaonongedwa  angakhalenso  zipembedzo  zina. Chifukwa  choti  Yazid  palibe  chomwe  amadziwa  za  dini  ya  chisilamu kwake  kudali kupanga  ntchito  yosalongosoka,  ngati  wina  akukanira  nkhaniyi  ayenera  kufufuza  umoyo  wa Yazid  mumabuku  odalilika.  Mapeto  antchitoyi   bwezi  Mulungu asakuchitiridwa  Ibadah.
Ndi uthenga  kwa  anthu  omwe  amapita  kukapanga  ziyarat  ku  manda   a Imam  Husain(a)  kuti  asafunikire kuti  azikongoletse  ndizovala  zabwino  kapena  kusamba   koma  kuti  atha  kupita  angakhale  ali  ndifumbi  chifukwa  choti    munthu  yemwe  adagona  pamalopo  ndi oti  adagwa  pansi  ndiponso  adali  fumbi lokhalokha  chifukwa  cha  anthu  osaopa  Mulungu  amenewa.
Ziyaratu  ashura  ndiya nthawi  zonse  ndi  chifukwa chake  amanena  kuti  (( كلّ يوم عاشورا  وكلّ أرض  كربلا ))  (tsiku lina lililonse  ndi  ashura pomwe  malo ena  alionse  ndi karibala)) kunena  kuti   munthu akakhala  pachisangalalo  kaya  madandaulo  ayenera  kumukumbukira  Imam  Husain (a),  kaya  likhala lachisanu,  Eidul fitir,  Eidul Quruban, tsiku la  Arafat  ayenera  kuwerenga  ziyaratu  ashura  komwe  ndikukumbukira  Imam Husain(a).
Mwina  wina  atha  kunena  kuti  ine  ndili  pachisangalalo  cha  kubadwa  kwa  Imam  Mahdi choncho  ndiyenera  kukhala  osangalala  osati  kudandaula  ayi,  kodi  mwaiwala  kuti   Imam  Zaman (Mahdi) (a)  adanena  kuti ((لابكينّ  عليك صباحاً و مساءاً  حتى أموت))  ((chifukwa  choti   masiku  ndi nthawi  zidandichedwetsa  kuti  ndisapezeke  nthawiyi  ndidzakhala  ndikulira  (kulilira  Imam Husain)  kummawa  ndi  madzulo  ena  alionse mpaka  imfa yanga)). Kumasulira  kuti  Imam  Zaman  amakhala  akudandaula  za  imfa  ya Imam  Husain (a)  nthawi  zonse.
Mfundonso  ina  yomwe  ingapereke  kuzindikira  kwina    kuti  munthu  athe  kumudziwa  Imam  Husain(a)  kuti  kodi  adali  ndani ndi nkhani  ya  Mubahalah.
Mtumiki  atagwirizana  ndi  ena  mwa  abusa   kuti  adzabwere ndicholinga   choti  aonetsane  kuti kodi  ndindani  yemwe  ali pachilungamo  adagwirizana  zoti  wina  aliyense  abwere  ndi anthu akubanja  lake  ndipo  apemphe  tembelero  kuchokera  kwa  Mulungu  kuti  lipite  kwa   munthu  wabodza.  Zomwe  mapeto  ake  zidali zoti  Mtumiki  adapita kumaloku  ndi  Ali, Fatwima, Hasan  ndi  Husain(a) .  Komwe  kuli  kwauza  Asilamu  kuti  akubanja  kwake  ndi  anthu  omwe  adabwera nawowa.  Monga  momwe  Mulungu  akunenera  mu Quran  yolemekezeka  kuti:
(( فمن حاجّك  فيه من  بعد  ما جاءك  من  العلم  فقل  تعالوا  ندع  أبناءنا  و أبناءكم  و نساءنا و نساءكم  و أنفسنا و أنفسكم  ثمّ  نبتهل  وفنجعل لّعنة  الله  على الكاذبين )).
(( Munthu  yemwe  angalimbane  nawe  pambuyo  poti  kudziwa  ndikuzindikira  kwakufika  nena  kwa  iwo  kuti  bwerani   tiyitane  ana  athu  ndi  ana  anu,  akazi  athu  ndi  akazi  anu,ife  ndi   inu  kenako  tipemphe  tembelero  la Mulungu  kuti  likhale kwa  amene  ali  onama)).