zolankhula za nzeru za Imam Ridtha (a
zolankhula za nzeru za Imam Ridtha (a)
11-امام رضا (علیه السلام):
كلّما أحدث العباد من الذنوب ما لم يكونوا يعملون ، أحدث الله لهم من البلاء ما لم يكونوا يعرفون؛.
11. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Ngati akopolo aMulungu achita ndikubweretsa machimo omwe sadawayambe wachita kale Mulungu naye amubweretsera mavuto omwe ndikale lomwe sadakumane nawo.
-12قال علیه السلام:
صاحِبُ النِّعْمَةِ یَجِبُ اَن یُوَسِّعَ علی عیالِهِ؛.
12. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu amene ali pamtendere kuti Mulungu adamupatsa chuma ayenera kuchigawa pakati pa azibale ake kuti nawo chiwathandize pa moyo wawo.
-13قال علیه السلام:
إنّ الله يبغض القيل والقـال و إضـاعة المـال و كثـرة السـؤال.
13. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Ndithu Mulungu amadana ndi mau oti “ kudanenedwa” ndi “ adati”, kuononga chuma ndi kuchulukitsa pempho.
-14عن رجل من اهل بلخ، قال:
كنت مع الرضا «عليه السلام» في سفره إلي خراسان، فدعا يوما بمائدة له، فجمع عليها مواليه من السودان و غيرهم. فقلت: جعلت فداك! لو عزلت لهؤلاء مائدة؟ فقال: «مه إنّ الرّبّ - تبارك و تعالي - واحد، و الأم واحدة، و الأب واحد، و الجزاء بالاعمال.
14. Munthu wina ochokera dera la Balikha adanena kuti: Tsiku lina ndidali ndi Imam Ridtha (A) mu ulendo wake opita ku Khurasan, tsiku lina adasonkhanitsa antchito ake onse akuda ndi oyera kuti akadye limodzi chakudya, ndidati kwa Imam: Mudakawapatsa iwowa chakudya chawo pa okha zidakakhala bwino, Imam adati: Khala chete, ndithu Mulungu wathu ndi m’modzi, bambo ndi mayi athu ndi amodzi (Adam ndi Hawa) ndipo mphoto ndi chilango chili kwa munthu wina aliyense molingana ndi ntchito zake.
-15قال عليه السّلام:
«اَلنَظَر اِليَ ذُريتِنّا عِبادَةٌ،
فَقيلَ لَهُ : يابنَ رَسُولِ اللهِ، النَّظَرُ اِليَ الاَئِمَةٍ مِنْكُمْ عِبادةٌ اَمْ اَلنَظُر اليَ جَميع ذُريةَ النبي عليه السّلام؟
فَقالَ: بَلِ اَلنَظُر اليَ جَميع ذُريةِ النَّبي عَبادَةٌ ما لَمْ يُفارِقُوا مِنهاجَهُ وَلَم يَتَلَوَّثوا بِالَمُعاصي.
15. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Kuyang’ana ana ndi zidzukulu zathu ndi Ibadah( kugwira ntchito yofunikira muchipembedzo komwe ndi kupembedza) , kudanenedwa kwa iye kuti: E! inu mwana wa Mtumiki, kodi kuyang’ana ana omwe ndi ma Imam (atsogoleri) ndikomwe kuli Ibadah kapena ana onse a Mtumiki? Adati: Kuyang’ana ana onse ndi Ibadah kufikira poti sadatuluke munjira ya Mtumiki ndipo sadalowelere m’machimo.
-16قال علیه السلام:
من أحب عاصياً فهو عاص و من أحب مطيعاً فهو مطيع و من أعان ظالماً فهو ظالم و من خذل ظالماً فهو عادلٌ. إنَّهُ ليس بين الله و بين أحد قرابة و لا تنال ولاية الله إلاّ بالطاعة؛
16. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu yemwe angamukonde munthu ochimwa nayenso ndi ochimwa, yemwe angamukonde oopa ndikumvera Mulungu nayenso ndi oopa ndikumvera Mulungu, yemwe angathandize opondereza nayenso ndi opondereza, yemwe angamuchepetse opondereza ndiye kuti ndiwachilungamo, ndithu pakati pa Mulungu ndi munthu palibe ubale ndipo kukhala pansi pa ulamuliro wake sikungapezeke pokha-pokha ndikumumvera iye.
-17قال علیه السلام:
اَلسَّخىُّ يَأكُلُ مِن طَعامِ النّاسِ لِيَأكُلوا مِن طَعامِهِ ، والبَخيلُ لا يَأكُلُ مِن طَعامِ النّاسِ لِئَلاّ يَأكُلوا مِن طَعامِهِ؛
17. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu owolowa manja amadya zakudya za anthu ena ndicholinga choti nawo anthu adzadye zakudya zake, pomwe munthu waumbombo samadya zakudya za anthu ena kuti anthu asadye zakudya zake .
-18قال علیه السلام:
عَظِّمُوا كبارَكم و صِلُوا أرحامكم فليس تَصِلوُنَهُم بشىءٍ أفضل من كف الاذى عنهم؛
18. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Alemekezeni ndi kuwakuza akulu-akulu anu ndipo lumikizani ubale pakati panu, kulumikiza ubale komwe kuli kwa bwino ndiko kusiya kuvutitsa azibale pakati panu.
-19سئل (عليه السلام):
أ تکون الارض و لا امام فيها؟ فقال (عليه السلام): إذاً لساخت بأهلها.
19. Imam Ridtha (A) adafunsidwa kuti: Kodi ndizotheka kuti pano padziko lapansi pakhale popanda Imam? Adati: Zikakhala choncho ndiye kuti nthaka ingameze okhalamo ( kusonyeza kuti padziko lapansi payenera kupezeka Imam nthawi zonse).
-20قال عليه السلام:
مَن استغفر الله بلسانه و لم يندم بقلبه فقد استهزأ بنفسه.
و مَن سأل الله التوفيق و لم يجتهد فقد استهزأ بنفسه.
و من سأل الله الجنة و لم يصبر علي الشدائد فقد استهزأ بنفسه.
و من تَعَوَّذَ بالله مِنَ النار و لم يترك شهوات الدنيا فقد استهزأ بنفسه.
و من ذكر الموت و لم يَستَعِدَّ له فقد استهزأ بنفسه.
و من ذكر الله تعالي و لم يَشتَق الي لقائه فقد استهزأ بنفسه.
20. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu yemwe angapemphe chikhululuko popanda kudandaula ndikunong’oneza bondo mumtima mwake wazinyozetsa yekha, munthu yemwe angapemphe kupambana ndi chikwaniritso popanda kulimbikira wazinyozetsa yekha, yemwe angamupemphe Mulungu mtendere popanda kupirira kumavuto ndi mazunzo wazinyozetsa yekha, yemwe angathawire kwa Mulungu pothawa moto wa Jahannma popanda kusiya zofuna zamtima wake wazinyozetsa yekha, yemwe angayikumbukire imfa popanda kuyikonzekera wazinyozetsa yekha, Yemwe angamukumbukire Mulungu popanda kulaka-laka kuti adzakumane naye wazinyozetsa yekha.
-21قال امام الرضا علیه السلام:
لیس العبادة كثرة الصیام و الصلاة، و انما العبادة كثرة التفكر فی أمر الله؛
21. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Kupembedza sikuchulukitsa kusala kokha basi kapena kupemphera swala kokha koma kuti kupembedza ndikuchulukitsa kuganiza zokhudza Mulungu.
22- قال علیه السلام:
صديق كل امرء عقله و عدوّه جهله.
22. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Nzake wa munthu wina aliyense ndi nzeru zake pomwe mdani wake ndi umbuli wake.
23- سئل علیه السلام عن خیـار العبـاد؟ فقــال(علیه السلام):
الذیـن إذا أحسنوا استبشروا, إذا أساؤوا استغفروا و إذا أعطوا شکـروا, و إذا ابتلو صبروا, و إذا غضبوا عفوا.
23. Adafunsidwa za akapolo a Mulungu omwe ndi abwino kuposa ena , Imam adayankha: Akapolo oti akagwira ntchito yabwino azisangalala nayo, akagwira ntchito yoyipa azipempha chikhululuko , akapatsidwa chinthu azithokoza, akamugwera mavuto azipirira ndipo akapsa mtima azikhululuka.
-24قال علیه السلام:
إنَّ الَّذِی یَطْلُبُ مِنْ فَضْلٍ یَکُفُّ بِهِ عِیَالَهُ أَعْظَمُ أَجْراً مِنَ الْمُجَاهِدِ فِی سَبِیلِ اللَّهِ؛
24. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Ndithudi munthu yemwe amalimbikira kufuna-funa zinthu zoti banja lake lithandizike nazo (chuma ndi zina) ali ndimalipiro akulu kuposa munthu yemwe angalimbikire munjira ya Mulungu.
-25قال علیه السلام:
يأتـى علـى الناس زمـان تكون العافية فيه عشرة أجزاء: تسعة منها فى اعتزال الناس و واحد فى الصمت.
25. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Idzafika nthawi kwa anthu yomwe mtendere udzakhala ndi magawo okwana khumi, magawo okwana asanu ndi anayi adzakhala ochotsa anthu pomwe gawo limodzi lidzakhala la kukhala chete.
-26قال علیه السلام:
ليـس لبخيل راحة, و لا لحسـود لذة و لا لملـوك وفـاء ولا لكذوب مــروة.
26. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu waumbombo alibe mtendere, munthu wa nsanje alibe kuzuna, atsogoleri alibe chilungamo ndipo munthu wabodza sakhala owolowa manja.
-27قال علیه السلام:
«أَلاَخُ الاَكْبَرُ بِمَنْزِلَةِ الاْأبِ».
27. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Mwana wamkulu ali ndi udindo ofanana ndi wa bambo ake.
-28روی عن عبدالعظیم، عَنْ أَبِی الْحَسَنِ الرِّضَا(علیه السلام) قَالَ: «یَا عَبْدَ الْعَظِیمِ! أَبْلِغْ عَنِّی أَوْلِیَائِیَ السَّلَامَ وَ قُلْ لَهُمْ أَنْ لَا یَجْعَلُوا لِلشَّیْطَانِ عَلَى أَنْفُسِهِمْ سَبِیلًا وَ مُرْهُمْ بِالصِّدْقِ فِی الْحَدِیثِ وَ أَدَاءِ الْأَمَانَةِ وَ مُرْهُمْ بِالسُّکُوتِ وَ تَرْکِ الْجِدَالِ فِیمَا لَا یَعْنِیهِمْ وَ إِقْبَالِ بَعْضِهِمْ عَلَى بَعْضٍ وَ الْمُزَاوَرَةِ فَإِنَّ ذَلِکَ قُرْبَةٌ إِلَیَّ وَ لَا یَشْتَغِلُوا أَنْفُسَهُمْ بِتَمْزِیقِ بَعْضِهِمْ بَعْضاً فَإِنِّی آلَیْتُ عَلَى نَفْسِی إِنَّهُ مَنْ فَعَلَ ذَلِکَ وَ أَسْخَطَ وَلِیّاً مِنْ أَوْلِیَائِی دَعَوْتُ اللهَ لِیُعَذِّبَهُ فِی الدُّنْیَا أَشَدَّ الْعَذَابِ وَ کَانَ فِی الْآخِرَةِ مِنَ الْخاسِرِینَ»؛
28. Nkhani idachokera kwa Abdul Adthim, iye adamva Imam Ridtha (A) akunena kuti: E! iwe Abdul Adthim ukandiperekere salaam kwa anthu ondikonda ndipo ukawauze kuti asalole satana kupeza njira mwa iwo, ukawalamule kuti akhale olankhula zoona ndi kusamala katundu wa anthu ndikubweza kwa eni ake, ukawalamule kuti akakhale ofatsa ndikukhala chete, kusiya kulankhulana ndikukambirana zinthu zomwe sizikuwakhudza, ukawalamule kuti akakhale oyenderana wina ndi nzake chifukwa ntchito imeneyi imapangitsa kuti ayandikire kwa ine, asakatanganidwe ndi kubalalitsa wina ndi nzake ndikuwadanitsa pakati pawo, chifukwa ine ndalumbira kuti munthu yemwe angapange zimenezi ndikumukwiyitsa m’modzi mwa azinzanga ndikupempha Mulungu kuti amupatse mavuto akulu padziko lapansi pano ndipo akakhale oluza tsiku lomaliza.
-29قال علیه السلام:
من القی جلباب الحیاء فلا غیبة له.
29. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Munthu yemwe angachotse chophimba cha manyazi kulankhula zoipa zake ndikololedwa.
-30قال علیه السلام:
لاتدعوا العمـل الصالـح و الاجتهاد فى العبادة اتکالا على حب آل محمد (صلی الله علیه و آله و سلم) و لا تدعوا حب آل محمـد(صلی الله علیه و آله و سلم) لامرهـم اتکـالا علـى العبـادة فـانـه لایقـبل احـدهـمـا دون الاخر.
30. Imam Ridtha (A) adanena kuti: Musasiye kugwira ntchito zabwino, kulimbikira kupembedza mukulingalira chikondi cha Akunyumba ya Mtumiki (s.a.w.w), musasiye kuwakonda Akunyumba ya Mtumiki (s.a.w.w) mukulingalira kupembedza chifukwa chimodzi mwa izo sichivomerezeka popanda chinzake.
Add new comment