Uthenga wa mtsogoleri wamkulu wa dziko la Iran(Khamenei) pa zochitika za haji.

Uthenga wa mtsogoleri wamkulu wa dziko la Iran(Khamenei) pa zochitika za haji.

 

Hazrat  Ayatullah  Khamenei  mtsogoleri  wamkulu wa kusinthika  kwa  chisilamu (Inqilabu Islami)  pa  mwambo  waukulu okhudzana  nkhani ya haji  wapereka  uthenga  oti  kufika  kwa  nthawi  ya  haji  imeneyi  ndi  chisangalalo chachikulu  kwa  asilamu onse  komanso  ndi  mpata  kwa  iwo  kuti  athe kuthetsa  mavuto  omwe  alipo  pakati  pa dziko  la  chisilamu  limeneli  lomwe  lili loti limatha  kukumana  ndi mavuto  nthawi  zambiri.Tsogoleriyu  walimbikitsa  asilamu  pankhani  yolimbikira  pofuna  kulimbana  ndi  gulu lozikweza lomwe  likufuna  kuchotsa  ndikuthetsa  chisilamu ndi kutukuka kwake  komanso kuchotsa  mfundo  ndi njira  zomwe zilipo  pofuna  kuwombola palestine ndi  asilamu  kuchokera  mmanja  mwawo  monga  makanema  onena  ndikupanga  zoipa  a zionism ndi ena. Iye  mukulankhula  kwake  wanena  kuti:  Ubale  ndi  mgwirizano  wa  asilamu  wagona  pankhani  ya  Tauhid( kusonyeza  kuti  asilamu  onse  ayenera  kukhulupirira  kuti  ndi Mulungu  yekha  yemwe  tingathe  kumuyang’ana  ndikumugwadira) komanso  kumudziwa  mdani  ndikulimbana  naye  ndi chimodzi  mwa  ziphunzitso zikulu-zikulu za  mwambo  wa haji  komanso  kuonjezera  apo  chiphunzitso cha  kudziwa mmene  dziko  likuyendera  lero  lino.

Uthenga  onse wamkuluyu  uli motere:

Mudzina la  Mulungu  mwini  chifundo  ndichisoni  chosatha

Kuyamikidwa  konse ndikwa  Mulungu ndipo  mtendere  ndi madalitso  akhale  kwa  bwana  wa  Atumiki  onse (s.a.aw)  ndi  akunyumba kwake  omwe  ali  anthu  abwino  komanso  oyenera  kulankhulana  nawo  osankhidwa.

Kufika  kwa  mwambo  wa haji  umenewu  ndipofunikira  kuti  asilamu  akutenge kukhala  chisangalalalo  chachikulu  kwa  iwo  komanso ndi mtendere ndi  mpata  omwe  wabwera  kwa  iwo  mumasiku ndi  zaka zimenezi. Mwachoncho  ndipofunika  kuti  asilamu  agwiritse  ntchito  mpata  umenewu  ndikuzindikira  kufunikira  kwake  chifukwa  kudzera  mu  haji  imeneyi  mavuto achisilamu adzachepetsedwa  ndikuchizidwa. Haji  ndi chitsime  cha mtendere wa Mulungu    choncho  inu  amene  mwapeza  mwayi  opita  ku haji  muli muchisangalalo ndi mtendere wa Mulunguwu. Padakali  pano  mwavomera  kuitana  kwapamwamba kumeneku   kuti  muzochitika  za mwambowu muthe  kuzitsuka  mitima  yanu ndikukhala  anthu  abwino  ndi mngwiro. Muyenera  kutenga  mtendere ndi kulemekezeka  kuchokera  ku bank  imeneyi  ndikuthandizika  moyo  wanu onse  pophunzira  izi: Kuzichepetsa  ndikugonjera  ku malamulo a Mulungu,  kuvomereza udindo  omwe  muli  nawo, kutakataka  pa nkhani  ya chipembedzo ndi  dziko,kulolerana  ndi kukhululukirana  wina ndi mnzake,kuzidalira  munthu  pofuna kupanga  zinthu zovuta, kudalira  Mulungu muchithandizo,kulankhula  pang’ono, kuzikhonza  ndi kutha  kukhalirana  ndi asilamu  ena. Mutha  kuphunzira  zinthu  zosiyana siyana  zokhudzana  chipembedzo  cha  chisilamuchi  ndikwatengera  anthu  ena  omwe  mwasiya  kwanu  ngati  mphatso. Asilamu  lero  lino  akufunikira  anthu omwe  kuganiza  ndi  ntchito  zawo  zikuchokera  pa  chikhulupiriro ndikuziyeretsa komanso  ndikuti  ayenera  kukhala  olimbana  ndi adani  ndikuyetsetsa kuziyeretsa mtima. Ntchito iyi  idzatha  kupulumutsa  mtundu wachisilamu kuchokera  ku mavuto  omwe  chisilamu  chimakumana  nawo moonekera  kapena  mobisika ndi  adani. Ndizosakaikitsa kuti  mtundu  wa nthawi  ino  ndi oti  uli mmaso  komanso  ozindikira  angakhale  asilamu  omwe  choncho  choona  chake  ndichoti  maiko  ambiri  achisilamu  akumana  ndikhaniyi  ndipo  inu mutha  kuona  zimenezi  pa nthawi yomwe  muli  kuhajiyi.  Kuchokera  muzinthu  izi zomwe  zilikuchokera  pa  chikhulupiriro ndi kuyezamira  kwa  Mulungu  ndi  momwe  asilamu atha  kukhala  opambana  ndikupita  patsogolo ndi  zolinga  zawo. Magulu  olimbana  ndikudzuka  kwa  chisilamu  akuyetsetsa  kufuna  kugonjetsa  asilamu  pogwiritsa  ntchito  zida zomwe  alinazo monga,kuchotsa  chitetezo,  kusokoneza kuganiza kwa  anthu  ndi  nzeru  zawo, kusokoneza magulu  ankhondo, chuma, kufalitsa  uthenga ndi  zina. Nkhaniyi  itha kumveka  bwino  kwa  inu  ngati  mutaona mmene maiko  akummawa  kwa  Asia  monga pakistan,Afghanistan, Syria, Iraq, Palestine ndi  maiko  amphepete  mwa  khaliji Faris  komanso  kumpoto  kwa  Africa monga  Libya,Egypt,Tunisia mpaka  Sudan ndi ena komanso  nkhondo  za  mmaiko, kunyozana  kwa  mipingo  ya chisilamu, kusakhazikika  kwa ndale, ziwembu  ndikulimba mtima  kwa  anthu ena, kupezeka  kwa  magulu  ena  opsola  muyezo  popanga  zinthu ndikupanda  umunthu  omwe  akutumbula zidali  za  anthu ndikutafuna  mitima  yawo ndi mano, anthu  okhala  ndi  zida omwe  akumapha  akazi  ndi ana ndikutenga  amuna  ndikukamawazunza  mosiyanasiyana. Zodandaulitsa  ndikumvetsa  chisoni  ndizoti  anthu  oterewa  akumanena  kuti  ndi  asilamu. Koma  zonsezi  zikuchitika  ndi anthu  omwe ali  ozikweza ndiotsatira satana  omwe  akupezeka  maiko  ambiri  lero  lino,  anthuwa  ndi omwe  akuipitsa  tsogolo ndikuononga  umoyo  wa anthu. Mukakhalidwe  ngati  aka  tisayembekezere  kuti  maiko  achisilamu  apita  patsogolo  ndichitukuko,  maphunziro  ndikudzuka  kuchokera  mtulo  lomwe  ali  nalo. Mchitidwe  ngati  uwu  upangitsa  kuti  kudzuka  kwa  chisilamu  kulephereke komanso  ndikusowetsa  chiyembekezo cha  kudzukaku  mpaka  kufikira  zaka zambiri.  Nkhani  yofuna  kupulumutsa  Palestine ndi  asilamu  ena  kuchokera  mmanja mwa  Zionist ndi  America idzaiwalika  pakati  pawo.

Nkhani  yofuna  kuthetsa  mavutowa nditha  kungogawa  pawiri yomwe  ikuchokera  pa mwambo  umenewu wa haji:

Choyamba: mgwirizano  wa  asilamu kuchokera pa umodzi wa Mulungu (Tauhid).

Chachiwiri: kumudziwa  mdani ndikulimbana ndi njira  zake pofuna  kulimbana ndi  chisilamu.

Kulimbikitsa ubale  ndichiphunzitso  chachikulu mumwambo wahaji umenewu. Nkhani  ikafika  apa  ndiye  kuti  kulankhulana  ndikukambirana  nkhani  zachipembedzo  mokhala  ngati  mukulimbana  wina  ndi mnzake  ndikoletsedwa. Kuvala  zovala  zofanana, ntchito  yofanana,kuyenda  kofanana, khalidwe lofanana ndilachikondi  nditanthauzo la  chikhulupiriro  cha  umodzi  wa  Mulungu  kwa  asilamu onse. Uwu  ndi tsutso  wa chisilamu  kwa  maganizo  ndichikhulupiriro  cha mtundu omwe  taulongosola  omwe  ndi owonongeka omwe  asilamu  onse  ayenera  kudziwa  kuti mtunduwu uli kunja  kwa  chisilamu. Asilamu  ayenera  kudziwa  kuti  chida  chomwe  angathe  kukudzumula nacho anthu amaganizo  ngati awa  omwe  akuphetsa  ndikuketsa  mwazi  wa  asilamu  ndi  anthu  osalakwa  ndi  mwambo  wa  haji  umenewu. Zodabwitsa  ndizoti  anthu  omwe  mwambo  wakuzitsuka  kuchokera  kwa anthu  ophatikiza  Mulungu  ndi zinthu  zina umenewu  omwenso  ndi  ntchito  ya  Mtumiki(s.a.aw), akupanga  kukambirana  pankhani  ngati  zimenezi  kukhala  zoletsedwa (haraam).

Ine  monga  tsogoleri wa asilamu monganso  atsogoleri  ena  achisilamu  ndikulengeza  kuti  zolankhula, ntchito zomwe  zingapangitse kusiyana  maganizo  pakati  pa asilamu  ndikukolezera moto komanso  kunyoza  zinthu zoyeretsedwa  za  gulu lina  lilonse la  chisilamu kapena  kukanira  gulu lina  lililonse  la  chisilamu, kuthandizira  magulu  okanira  ndi ophatikiza  Mulungu, kuchita  chipongwe  chisilamu lamulo lake  ndi  haraam.

Kumudziwa mdani  ndi nsichi yachiwiri  yomwe sifunikira kuyiwalidwa ndipo nthawi  yomwe  tikuponya  miyala pamwambo  wa  rajimu  jamrat  tiyenera  kukumbukira  nsichi imeneyi.

Choyamba  kupezeka  kwa  mdani  pakati  pathu  kusatipangitse  kuiwala  nkhaniyi. Chachiwiri  ndichoti  kumudziwa  mdani lero lino ndi makanema  ama Zionists  ndi  anthu  ozikweza  omwewa  moti sipakufunikira  kuti tilakwitse  chilichonse  pankhaniyi. Chachitatu  ndichoti  njira  za  anthuwa  ndiko  kubweretsa kugawikana  pakati pa  asilamu, kufalitsa  ntchito zoipa,ndale  zosakhala  bwino,chuma ndi  zina.

Chimene  iwo  ayenera  kudziwa  ndichoti ife  asilamu sitibwerera  mmbuyo  muchifuniro  cha  Mulungu koma  tipitiriza  kulimbana  nawo, koma  tikayiwala  adaniwa  ndiye  kuti ntchito  yathu idzatikulira  kwambiri.

Ine  ndili  ndichikhulupiriro  kuti  nkhani yolimbana  ndi  adaniwa muno  dziko la  Iran  taiona ndipo  zinatheka  chifukwa  choti  chilingaliro  chathu  ndi kugwira  ntchito  kwathu  kudali kusatopetsa.Inunso  asilamu  azathu amaiko  ena  muyeneranso  kugwiritsa  ntchito ndikutengera  nzeru pankhaniyi.

Pomaliza  ndikupempha  Mulungu  kuti  adalitse haji  imeneyi ndikuti  ikhale njira  yothetsera  zolinga  za adani ndikuti  Mulungu  avomere ndikulandira  haji  yanu  komanso  kukupatsani matupi ndi  moyo  wathanzi.

Wasalamu alaikum warahamatullah ta’ala  wabarakatuh.

Sayyid Ali Khamenei

5 dthili hijjah,1434, mofanana ndi 19, mihir 1392.

 

 

 

 

Add new comment