Kodi wahabi ndi ndani? 2

Kodi wahabi ndi ndani? 2
Bismillahi rahmani rahim
Salam alaikum
Ndiri ndi chikhulupiliro kuti muli ndi umoyo wabwino.
Mutu wathu waukulu wa nkhani pano, ndi kuchilongosola ndi kuchikuchidziwitsa chisilamu kwa ena. Koma mukukambirana komwe kwadutsa, talongosolapo kuti gulu la Wahabi ndilomwe latenga gawo lalikulu pofalitsa chisilamu mwa pamwamba(kunja kwa chisilamu) osati momwe chisilamucho chiliri.
Ndipo zikhulupiliro za gululi zalongosoledwa ngakhale kuti pamwamba limawoneka ngati ndi gulu la chisilamu koma ndi gulu lomwe lidachita kupangidwa ndi adani komanso ndi losiyana ndi chipembedzo cha chisilamu.
Ngati muli ndi chikhulupiliro chenicheni kuti mwapeza chisilamu chowonadi, tachenjeza kale kuti pofunika kukhala ochenjera ndi atcheru kwambiri ndi cholinga choti musapusisidwe ndi magulu omwe ali osocheletsa mudzina la chisilamu, ndi cholinga choti musasochere.
Mukukambirana kwathu lero, tikufuna tilongosole bwino zomwe tanena kale zokhudzana ndi gulu la Wahabi, kufikira kuti titadziwa bwino zokhudza gulu limeneli ndikutinso muthe kudziwa kuti ndichifukwa chiyani gulu la Wahabi likusiyana ndi chipembedzo cha chisilamu.
Nkhani yokhudzana ndi gulu la Wahabi komanso kapezedwe kawo mphamvu zolamulira ndi kayambidwe kake ndi yodabwitsa ndinso yodandaulitsa kwambiri. Kapolo ine ndikuganiza kuti ndicholinga choti nkhani imeneyi ikhale yosavuta komanso yomveka bwino, zingatithandize kwambiri titawerenga mbiri ya umoyo wa Ibn Taymiyyah, Muhammad Abdul Wahaab ndi aliyense yemwe adapitiliza njira ya Muhammad Abdul Wahaab.
Ndikuganiza kuti inu nokha mutayika nthawi yanu ndikuwerenga zokhudzana ndi anthu amenewa zingakhale bwino kwambiri.
Mwachoncho kapolo ine mukukambirana kwathu kochepaku, ndidzakulongosolerani pang’ono za mbiri ya kayambidwe ka gululi ndi zinanso zoipa zomwe akhala akupanga. Konseku tikufuna kuti muyeso oyesela ubwino ndi kuipa kwa gulu limeneli ukhale m’manja mwanu kuti mudzathe kusiyanitsa gulu la Wahabi kuchokera ku chisilimu.
Mwachoncho ngati muyeso umene mudzapatsidwawu ukhale m’manja mwanu mudzatha kuwadziwa bwino lomwe anthu omwe avala chovala cha chisilamu mwabodza ndikumati akugwira ntchito posakhala mudzina la Wahabi koma ali Wahabi kumene.
Ndichifukwa chiyani padakali pano gulu la Wahabi likugwira ntchito zake kudutsira muchovala chomwe sichili chake?
Poyamba tiyenera kudziwa izi kuti pali ma Hadith omwe adatipeza ife kuchokera kwa mtumiki wa Mulungu okondedwa omwe tikamawafananiza ndi gulu la Wahabi, amachita kugwirizana kwambiri.
Mubukhu la Swahih Bukhari, volume 1/ tsamba 351/hadith 990, gawo la Istithqau/ babu 26. zidanenedwa kuchokera kwa Abdullah Ibn Umar ndipo iye adamva kuchokera kwa mtumiki (s.a.a.w) akuti: “ee! Mulungu wanga ikani madela a Siriya ndi Yemen kukhala odalitsika kwa ife”.
Omutsatira mtumiki adafunsa kokwana katatu kuti: “ee! Mtumiki waMulungu, nanga dela la Najd (lomwe likupezeka ku Saudi) lidzakhala bwanji?
Ndikuganiza kuti kadali kachitatu, Mtumiki (s.a.a.w) poyankha adati; “dela la Najd ndi dela la chivomerezi ndi Fitna (ukamberembere) ndipo kumeneko ndikomwe kudzawonekera nyanga za Satana”.
عن ابن عمر قال اللهم بارک لنا فی شامنا اللهم بارک لنا فی یمننا .قالوا وفی نجدنا . فاظنه قال فی الثالثه : هناک الزلازل و الفتن و بها یطلع قرن الشیطان
Aainiy yemwe ali mulembi wa bukhu la Umdatu al-Qariy bukhu lomwe likulongosola bwino bukhu la Swahih Bukhariy mu volume 7/ tsamba 59 adalemba kuti;  “ mawu oti (nyanga ya Satana) akutanthauza kuti gulu la Satana”.

و بنجد یطلع قرن الشیطان ای امته و حزبه
Inu tangowonani mu chaka cha 1987 mutsiku lachisanu lamagazi m’mwezi wa Muharram, mwezi omwe ngakhale kupanga nkhondo (Jihad) ndikosaloledwa, pamalo omwe ali abwino kwambiri kuposa malo ena aliwonse, malo omwe ngakhale kupha chinyama kumene ndi kosaloledwa, kodi malo ngati amenewa muchaka chimenechi ndi magazi a anthu oponderezedwa komanso osowa chitetezo angati adakhetsedwa? Anthu ophedwawa adapita ku Makkah ndicholinga chokapanga mapemphero okakamizidwa a Mulungu ndipo adafera munjira ya Mulungu.
Zikunenedwa kuchokera kwa mtumiki wachisilamu olemekezeka (s.a.a.w) mubukhu la Swahih Bukhariy volume 6/ tsamba 2748/ hadith 7123/ gawo la Tawhid/ babu 57 (Qiraatu al-Faajir wal-Munaafiq).
Said Khudriy adamva mtumiki wachisilamu (s.a.a.w)  akunena kuti;
“kudzabwera anthu kuchokera kudela la kum’mawa omwe azidzangowerenga Qur’an, koma sadzakhala ogwiritsa ntchito zonena za Qur’an ndipo palibe chomwe adzapindula kuchokera mu Qur’an. Gulu limeneli lidzatuluka muchipembedzo ngati momwe muvi umachokera  pa uta ndipo osabweleranso. Anthu adamufunsa mtumiki wachisilamu (s.a.a.w) kuti; “kodi gulu limeneli lili ndi chizindikiro chanji?”
Mtumiki poyankha adati; “chimodzi mwa zizindikiro za gulu limeneli ndi kumeta mpala.

یخرج ناس من قبل المشرق و یقرءون القرآن لا یجاوز تراقیهم یمرقون من الدین کما یمرق السهم من الرمیه ثم لا یعودون فیه حتی یعود السهم الی فوقه .
قیل ما سیماهم .
قال سیماهم التحلیق او قال التسبید .

Mwachoncho ena mwa ma Sheikh ndi ma Ulama akuluakulu adati Hadithiyi ikukwanira pofuna kudziwitsa ubodza wa gulu la Wahabi chifukwa choti iwo amawalamula ndi kuwakakamiza otsatira awo kuti azimeta mitu yawo. Ndipo pa magulu achisilamu palibe munthu kapena gulu lomwe limakakamiza (Wajib) otsatira ake kuti azimeta mitu yawo ndipo lamulo lometa mpala ndi lamulo lomwe amangopereka ma Wahabi okha kwa otsatira awo basi kuti nthawi zonse azimeta mpala.
Mpakana Ahamad Zainiy Dehlan akulongosola mu bukhu la Fiqh al-Wahabiyah/ tsamba 19 kuti; Muhammad Ibn Abdul Wahaab (mtsogoleri wa gululi) adalamula mkazi wina kuti amete mutu wake. Mkaziyo adayankha nati, iwe amene ukuti akazi ndi oyenera kuti azimeta mitu yawo, uyenera kupelekanso lamulo loti amuna azimetanso ndevu zawo chifukwa choti ndevu za amuna zilingati tsitsi la akazi lomwe limatengedwa kuti ndi chikongoletso kwa iwo. Muhammad Ibn Abdul Wahaab adasowa chonena ndi kuyankha kwa mkazi ameneyu.
Oyamba kuchokera mwa omwe adatsutsana ndi kusemphana ndi Muhammad Ibn Abdul Wahaab adali bambo ake ndi mchimwene wake. Ndipo mchimwene wake adalemba bukhu lotsutsa zikhulupiliro zake. Mpakana pambuyo pamkangano ndi kusemphana maganizo ndi awiriwa iye (Muhamma Ibn Abdul Wahaab) adathawira ku Madinah.
Chiphunzitso cha Wahaabiy chidayamba kupeza mphamvu komweko pomwe Muhammad Ibn Abdul Wahaab adagwirizana ndi Muhammad Ibn Saud. Kutanthauza kuti zikhulupiliro, lamulo lakupha anthu ena osakhala iwo, ndi zina zoipa zimanenedwa ndi iye ndipo zimachitika ndi Muhammad Ibn Saud.
Apa ndi pomwe padayambikira ulamuliro wa gulu la Wahaabiy ku banja la Saud (mudziko la Saud Arabia).
Tangowonani tsankho lomwe mtundu wa Saudi ulinalo. Ndicholinga choti yemwe adzalamulire dzikoli adzangokhala ochokera ku mtundu umenewu, iwo adasintha dzina la dzikoli lomwe linkadziwika ndi dzina loti Hijaz ndikuyika dzina loti Almamulakatul Arabiyyatu al-saudiyyah (dziko lomwe likulamuliridwa ndi Aluya ochokera ku mtundu wa Saudi). Kutanthauza kuti munthu wina ochokera mudziko limeneli ngati siali ochokera ku mtundu umenewu sangathe kukhala mtsogoleri wadzikoli
Ngati tikufuna kungowonapo pang’ono zoipa zomwe gulu limeneli lidapanga, titha kulongosolapo izi:
Kupha komwe adapanga mu dela la Twaif mpakana anthu adautcha mzinda omwe udachitika zimenezi kuti “Mzinda wa mizimu”. Anadula mitu ya anthu onse mpakana ana oyamwa kumene omwe adali m’manja mwa amayi awo adawadula mitu. Nkhani imeneyi idalembedwa ndi Ahmad Zainiy Dehlan pa tsamba 45 kuchokera mu bukhu la Duraru al-Sunniyah fi Radd Alal Wahabiyah .
Ahmad Zainiy Dehlan adalemba kuti iwo (Wahabi) adamupha munthu opanga Adhana yemwe adali osawona chifukwa chomufunira zabwino mtumiki wachisilamu (s.a.a.w).
Mu bukhu la Ta’ariikhu al-Saudiyyah tsamba 126 polongosola zoipa za gulu la Wahabi muchaka cha 1795. Gulu la Wahaabiy motsogozedwa ndi Saud Ibn Abdul Aziz adanyamuka ndi gulu lankhondo lokwana 12000 kukaphwasula mzinda wa Karbala ndipo adapha anthu omwe adali asilamu okwana 3000 ndinso adawononga ndi kugumula manda a chidzukulu cha mtumiki wathu (s.a.a.w) yemwe ali Husein mwana wa Ali (a.s) ndikuba zomwe zidali pamandapo.
Muchaka cha 1797 ma Wahabi uku akuyimba ndi kuvina adayamba kuphwasula ndi kuwononga zizindikiro zoyeretsedwa za chisilamu. Iwo adaphwanya malo omwe mtumiki (s.a.a.w) adabadwirapo mu dela la Mualla adaphwanyanso malo omwe olemekezeka Khadijah (a.s) adabadwirapo ndinso malo ambiri akuluakulu a chisilamu. Zonsezi kumachita kuti amakhala akuyesetsa kusunga zizindikiro za aYuda mudzina loti akusunga zinthu za mbiri ya kale (Museum).
Kodi pangakhalenso choipa china kuposera apa, pomwe adaphwanya nyumba ya olemekezeka Khadijah ndipo chonde mundikhulukire polongosola izi kuti adayisandutsa nyumbayo kukhala chimbudzi (adamangapo zimbudzi).
Malo omwe mtumiki (s.a.a.w) adabadwira adawasandutsa ndikukhala ogulitsirapo ziweto ndi zinyama.
Adawotcha malo akulu osungilako mabuku omwe adalibenso ofanana nawo ku Makka, omwe adali ndi mabuku m’mitu yosiyana siyana yokwana 60000, mudali mabuku okwana 40000 omwe adalembedwa ndi manja omwe adali chuma chachikulu kwambiri cha maphunziro.
Muchaka cha 1923 adaphwasula mzinda wa Madina ndikuwononga manda onse monga manda a Ibrahim mwana wa mtumiki wa chisilamu (s.a.a.w), akazi a mtumiki omwe amatengedwa kuti ndi amayi a anthu okhulupilira ndinso adawononga ndi kuphwanyanso manda a anthu akunyumba ya mtumiki (Ahalbait) monga manda a Imam Hasan (chidzukulu cha mtumiki), Imam Sajjad, Imam Baqir ndi Imam Swadiq (mtendere ndi madalitso a Mulungu akhale kwa iwo).
Ndipo ngati panopo tingawonetsetse, magulu akuluakulu a umbanda padziko pano monga Taliban, Alqaedah, gulu lowukira ulamulilo wa dziko la Siriya, nkhondo yomwe ikuchitika ku Pakisitan ndi anthu akupha komanso ambanda ndi opandukira akuluakulu monga Bin Ladin ndi Rigi, onse ali ndi chiphunzitso ndi chikhulupiliro cha Wahabi.
Ndichifukwa chiyani gulu limeneli lidapangidwa ndi maiko ozitukumulu ndi opondereza ndi kumathandizidwa?
Chifukwa dziko padakali pano lazindikira zowona za chisilamu chenicheni ndipo anthu akumayiko aku Ulaya ndi Amereka komanso ena omwe ali akhirisitu azindikira zowona za nkhani imeneyi kuti kodi chisilamu chiri ndi chuma cha pamwamba bwanji.
Kodi anthu amenewa ngati akufuna kudziwa zambiri ayenera kutani? Ayenera  kufufuza ndi kudziwa za chisilamu chenicheni.
Nanga ayenera kutani ngati akufuna kudziwa za chisilamu chenicheni? Ayenera kuyamba kufufuza za chisilamu kuchokera kumadela omwe chisilamu chidayambira kutanthauza kuti Makkah ndi Madina.
M’mayiko amenewa omwe chisilamu chidayambira, azawadziwa anthu omwe amaziwonetsa ngati asilamu enieni koma zowona zake asali asilamu.
 kodi zikatero chidzachitika ndi chiyani?
Mwadzidzidzi chilengedwe cha munthu chidzalankhula mokweza kuti mtundu wa anthu kapena gulu la chipembedzo lomwe lingamaganize ndi kumagwira ntchito chonchi ndiye kuti likunama komanso ndilosochera ndinso losocheretsa.
Gulu la Wahaabiy likupezeka ndi cholinga choti liwonetse chipembedzo cha chisilamu ngati kuti ndi chabodza ndinso cha nkhanza. Pofuna kuwaletsa anthu afulu ndi ofuna chilungamo kuti asakhale asilamu ndi cholinga chofunanso kuwasintha anthu oyera ndi abwino muchilengedwe kuti akhale ngati zida kapena zitsulo zomwe ziribe kuganiza ndi kuzindikira kwina kulikonse powapha anthu osalakwa.Inu tawonani zomwe akupanga anthu magulu awumbanda ndi achifwamba mu mayiko a pakisitani, Iraq ndi Siriya, akumazinga anthu osalakwa makosi ndi mpeni mudzina la Mulungu ndi kumati “Allah Akbar”.
Tafufuzani pa makina a Intaneti mawu oti (parachnar) kodi zidzakuwonekerani zithunzi zotani zakupha?
Ndi chifukwa chiyani anthu ophedwawa anyenyeka nyenyeka chonchi?
Ndi ndani awateketa chonchi?
Ndichifukwa chiyani awateketa chonchi?
Kodi lamulo lomwe likuperekedwa kwa akazi aku dziko la Tunisia likutanthauza chiyani? Omwe akulamulidwa kuti ndi dzina la Jihad azipita ku Siriya ndikumakapanga zadama ndi chiwelewele kuti awathandize ndi kuwapatsa mphamvu anthu owukira dziko lachisilamu la Siriya ndicholinga choti asapeleweredwe muchisangalalo cha thupi.
Kodi tanthauzo la Hadith ndakuwuzani ija mwaiwala kuti nyanga za Satana zidzawonekera?
Kodi ndi munthu wanji mfulu yemwe olo ndi pang’ono angalitenge gulu limeneli kuti ndi lachisilamu?
Zikomo kwambiri.   

Add new comment